12.0 MTENGO OWONETSA KUSASIYANA PAKATI PA ABAMBO, AMAYI, ACHINYAMATA NDI ACHITSIKANA PAKAGWILIDWE KA NTCHITO NDI KUGAWA PHINDU (GENDER BALANCE TREE)
Mtengowu umafotokozera za mgwirizano omwe umakhalapo pa banja, pa kagawidwe ka ntchito, phindu, umwini wa katundu ndi kupereka nawo maganizo. Mtengowu umafanizira zochitika pa banja ndipo thunthu likuimira anthu omwe ali m’banjamo, pomwe mizu ikuimira ntchito zomwe banjalo likugwira pomwe nthambi ndi zipatso zikuimira phindu.
Kusiyana pakagwiridwe ka ntchito pa banja kumalepheretsa anthu kuchita zofanana komanso kumapangitsa kugwira ntchito mwaulesi ndipo kusiyana pa kagawidwe ka phindu ndi umwini wa katundu kumachepetsa chidwi pa kagwiridwe ka ntchito zomwe zimabweretsa umphawi pa banja.
ZOLINGA ZA MTENGO OWONETSA KUSASIYANA PAKATI PA ABAMBO, AMAYI, ACHINYAMATA NDI ACHITSIKANA
Step 1: Kujambula Thunthu la mtengo
Thunthu la mtengo limaimila mmene khoma la munthu lilili. Mkati mwake bambo ndi mayi amajambulidwa ataima limodzi. Ana a akazi amajambulidwa pansi pa mayi ndipo ana a amuna pansi pa bambo. Mukamajambula banja, lionetse bwino lomwe kuti ndilotsogoleledwa ndi bambo, mayi kapena mwana, lionetsenso ngati lili la mitala
Step 2: Kujambula mitsitsi
Omwe akujambula ajambule mitsitsi iwirwi kuimila zochita za amayi ndi atsikana, mitsitsi ina iwirinso kuimila zochita za abambo ndi anyamata mbali ziwiri zosiyana komanso makaka (colour) yosiyana. Msitsi wina wa pakati oyimila zochita zomwe abambo ndi amayi ndi ana amatha kuchitira pamodzi. Kenako anthu azilemba ntchito mmitsitsiyi malingana ndi mafunso omwe awonetsedwa mu gawo la kagwiridwe ka ntchito. Ayenera kuonetsanso zochita zomwe zimatenga nthawi yambiri poziika mkati mwa bokosi lozunguira lakuda. Zochita zomwe zimabweretsa ndalama zochulukilapo zilembedwe mu bokosi la folokona. Msitsi wina wa pakati ndi oyimila zochita zomwe abambo ndi amayi ndi ana amatha kuchitira pamodzi.
Step 3: Kujambula nthambi ndi zipatso
Jambulani nthambi zisanu monga mwa mafunso afunsidwawo, nthambi ziwiri za momwe amayi ndi ena onse aakazi amagwiritsira ntchito ndalama pa khomopo, nthambi zinanso ziwiri za momwe abambo ndi ena onse aamuna amagwiritsira ntchito ndalama pa khomopo. Nthambi ya pakati ndi ya momwe abambo and amuna onse pakhomopo komanso amayi ndi azimayi onse pakhomopo amagwirotsira ntchito ndalama pamodzi ngati banja. Jambulani zizindikilo zoimila kagwiritsidwe ntchito ka ndalama kamene amayi ndi ena onse aakazi, abambo ndi ena onse aamuna amachitira ku mapeto kwa nthambi mbali zawo. Jambulani bokosi lozungulira lakuda la zomwe zikugwiritsa ntchito ndalama zochuluka ndipo mwaonapo kuti pakufunika kusintha ngati khomo. Pa thambi iliyonse mkati mwake jambulanimo momwe gulu lililonse pa banjapo likugwiritsira ntchito ndalama. Jambulani bokosi lozungulira lakuda la zomwe zikugwiritsa ntchito ndalama zochuluka ndipo mwaonapo kuti pakufunika kusintha ngati khomo. Pa nthambi yapakati pomwe pamajambulidwa zizindikilo za mmene tonse pamodzi timagwilitsira ntchito ndalama ngati banja, zizindikilo za pamenepa zimaikidwa motsamila kwambiri mabali imene imatsogola kugwiritsa ntchito ndalamazi. Bokosi la makona atatu (triangle) limajambulidwa kuzungulira magwiritsidwe ntchito a ndalama opindula omwe banja lonse likufuna apitilire.
Step 4: Kodi chomwe chimayendetsa/ kukankha mtengowu ndi chani? (Control over assets and decision-making)
Banja limaika zizindikilo za ziganizo zokhudza amuna kapena akazi ku mbali yawo yoyenera mu mtengowu, izi ndi monga umwini wa katundu yemwe mbali iliyonse ili naye monga malo, ziweto, nyumba. Banja limaika zizindikilo za ziganizo za amuna kapena akazi ku mbali yawo yoyenera mu mtengowu mokhuzana ndi udindo popanga ziganizo monga za amayi, za abambo, za anyamata, za atsikana. Moonjezerapo pamaikidwanso ziganizo zomwe zimapangidwa mogwirizana amuna ndi akazi.
Step 5: Nthawi ya zokambilana
Gulu lililonse limalongosola kwa anzawo onse pamodzi mmene alembera zinthu mu mtengo wawo kuti magulu ena ayikilepo ndemanga. Kenako gulu lonse pamodzi limajambula mtengo wa Jenda movomelezana ngati banja. Mtengo ojambulidwa mogwirizana ngati banjawu umapangidwa ndi cholinga choti nkhani zonse zofunika ziziwike, maphunziro onse ofunika aphunziridwe komanso zonse zoyenera kuti zikonzedwe ziwonekere pamtunda mothandizilidwa poyankha mafunso awa:
Mafunso othandizira mu ndondomekoyi
Step 6: Kuchitapo kanthu: Kodi choyenera kusintha ndi chani? (Household change commitments)
Jambulani bokosi lozungulira pa zinthu zomwe banja lonse lagwirizana kuti zikuchitika bwino (zosafunika kuti zisinthe) zomwe zikupangitsa kuti mtengo ukhale okomera banja lonse. Banja lonse ligwirizane zinthu zofunika kuti zichitike kuti mtengowu ukhale okomera aliyense ndipo izi zilembedwe ndi makaka obiliwira (green)
Banja liike chizindikiro chiimilira mmene mtengowu ukuonetsera kukondera kapena kukomera magulu ena pabanjapo. Banjalo likambilane kuti akuyenera kuchita chani kuti mtengo wa Jenda wawo ukhale okomera aliyense. Kodi ndi ntchito ziti zome ziyenera kugwiridwa mothandizana? Kodi asiye kugula zinthu ziti kuti ndalama zisamalike pakhomo? Kodi ndi katundu uti amene akuyenela kuti wina aliyense pakhomopo athe kugwilitsa ntchito momasuka? Pa nkhani za kapezedwe ka chuma, kodi atha kuwonjezera kapena kuchotserapo nthawi yomwe gulu lina likugwilira ntchito kuti phindu lichuluke?
Banja lonse pamodzi lipeze zinthu zisanu (5) zimene akufuna zipitilire kapena zichepe kuti mtengo wawo wa Jenda ufikile pokomera onse. Izi zilembedwe ndi makaka a green kapena zuthethedwe ndi makaka ofila (red) komanso chizindikiro chatsopano cha green pa malo oyenera.
Step 7: Kulemba bwino lomwe zomwe banja lagwilizana kuti lidzichita kuti lionetsetse kuti mtengo wawo wa Jenda ndi okomera aliyense nthawi zonse
Banja lililonse layenera kuti lizichita kawuniwuni wa mmene likutsatilira zonse zomwe agwilizana kuti mtengo wawo wa Jenda upitilire kukhala wokomera aliyense mwezi ndi mwezi. Pa mapeto pa maphunziro a mtengo wa Jenda wokomera aliyense, banja lililonse lilembe bwino lomwe zonse zomwe agwirizana ndi zoti zichitike kapena zisiyike kuti azitha kuziunika okha ngati zinthu zikuyenda pogwiritsa ntchito gawo lili mmusili.
ZIMENE BANJA LIKUFUNA KUSINTHA /KUKONZA KUTI MTENGO USAGWE (KUCHITA KAWUNIWUNI)
Chitsanzo cha kawuniwuni wa mfundo zomwe khomo latsimikiza
Dzina la banja: Bambo ndi Mai Phiri
Masomphenya a pa banja: Kukhala ndi khomo la chakudya chokwanira chaka chonse, nyumba yamalata komanso ng’ombe ziwiri
Tsiku lopangila kalondolondo: 20 August, 2022
Zomwe mukufuna kusintha pa Banja
|
Ntchito
|
Mlozo |
Zimene Banja lachitapo pakali pano
|
Ndemanga |
Kugawana kagwilidwe ka ntchito pa Banja
|
Kugwira ntchito za pa khomo
|
Abambo and anyamata kukwanilitsa ntchito yotunga mmadzi ndi ntchito zina za pakhomo |
Abambo akumatunga nawo madzi tsiku liri lonse
|
akazi akukhala ndi nthawi yogwira ntchito zobweretsa chuma ngati kulowa ma gulu osunga ndi bwereketsa ndalama
|
|
|
Anyamata akumatunga nawo madzi mwa apo ndi apo |
|
|
Kuchepetsa kagwilitsidwe ntchito ka ndalama pa zinthu zosafunikila |
Amayi kusiya kupanga njunga |
Malipoti a masiku omwe amayi anapita ku njunga |
Amayi asiyilatu Njunga |
Ndalama zomwe zasungidwa zagwilitsidwa ntchito kulipilila mwana sukulu |
Abambo kuchepetsa kumwa mowa |
Kuchuluka kwa masiku omwe abambo anapita kukamwa mowa |
Abambo akumwa mowa kamodzi pa mwezi |
Ndalama zomwe zasungidwa zagwilitsidwa ntchito yogulila zinthu zapakhomo ndi chakudya |