Module Articles

Maphunziro a GESI

Maphunziro a GESI

Mau Otsogolera

  1. Mau Otsogolera

JENDA

  • Ndi ntchito, ubale ndi udindo zimene zimapelekedwa kapena zimapatsidwa kwa abambo, amayi, anyamata ndi atsikana kutengela chikhalidwe, mtundu wa anthu komanso komwe tikuchokela.
  • Chikhalidwe chimalondoloza zinthu zomwe amuna kapena akazi akuyembekezeredwa kuti azichita m’deralo.
  • Kusiyana kwa ntchitozi kumadza kutengela maganizo ndi chikhalidwe cha mtundu wa anthu (zimachita kupangidwa)
  • Momwe tikugwilira tchito, ubale ndi udindo pakati pathu (Jenda) zimasintha mkupita kwa nthawi komanso zimasiyana kuchoka khomo ndi khomo, mtundu ndi mtundu, mudzi ndi mudzi etc

KUSASIYANA PAKATI PA AMUNA NDI AKAZI (GENDER EQUITY)

  • Kupereka mpata ofanana okhuza chitukuko, maudindo, ndi zida kapena zipangizo pakati pa abambo, amayi, anyamata ndi atsikana potengera luso ndi luntha lawo. Kupereka mpataku sikuyenera kuyang’ana kuti uyu ndi wamwamuna kapena wamkazi. Aliyense akhale ndi mwayi ofanana ndi mzake kuti akhonza kusankhidwa.
  • Kukhala ndi khalidwe la ngwiro poganizila mofanana pakapezedwe ndikagwilitsidwe ntchito ka zinthu posategera kuti uyu ndi mwamuna kapena mkazi.

Kusasiyana mu Jenda (gender equity)

KUFANANA PAKATI PA AMUNA NDI AKAZI (GENDER EQUALITY)

  • Kugwira ntchito ndi kugawana phindu, maudindo ndi zipangizo zogwirira ntchito mofanana pakati pa amayi, abambo, anyamata ndi asungwana, ndi magulu ena onse.
  • Kupeleka ulemu wokwanila kwa wina ndi nzake pakapezedwe, ulamuliro ndikagwilitsidwe ntchito ka zinthu pachitukuko ngati ulimi posatengela kuti munthuyo ndi mwamuna kapena mkazi.

Kufanana mu jenda (gender equality)

 KHUNGU PA NKHANI ZA JENDA (GENDER BLINDNESS)

  • Ndikusazindikila ndikugwilapo ntchito pazofuna za amayi, abambo, anyamata ndi asungwana, ndi magulu ena onse m’mudzi

 

 KUKHALA TCHELU PA ZA JENDA (GENDER SENSITIVITY)

  • Kukhala munthu wozindikila zofuna ndi zintchito za amayi, abambo, anyamata ndi asungwana, ndi magulu ena onse komanso kutha kuchitapo kanthu

 

 KUPHATIKIZIKA PA GULU (SOCIAL INCLUSION)

  • Kuphatikizika kwa anthu kumawonetsetsa kuti magulu onse ndi madera, kuphatikizapo amayi, abambo, achinyamata ndi olumala ali ndi mwayi wofanana powongolera zothandizira zachitukuko, mwayi wofanana kutenga nawo mbali popanga zisankho, ndipo akhoza kupindula mofanana ndi mapulogalamu a chitukuko.
  • Kuphatikizika ndi anthu ndi kupereka njira zambiri kwa anthu osowa kuti akhale ndi moyo wabwino.
  • Amafuna kuthana ndi kusalingana ndi/kapena kuchotsedwa kwa anthu omwe ali pachiwopsezo pokweza njira zotenga nawo gawo pagulu komanso kulimbikitsa mwayi, mwayi wopeza zinthu, mawu ndi kulemekeza ufulu wa anthu. Ikufuna kulimbikitsa kupatsa mphamvu ndi kupititsa patsogolo magulu amtendere ndi mabungwe onse.

 

KAFUKUFUKU/KAWUNIWUNI WA JENDA (GENDER ANALYSIS)

  • Kafukufuku kapena kawuniwuni wa jenda amaona ntchito ndi ma udindo omwe amapelekedwa kwa abambo, amayi, anyamata, atsikana ndi magulu ena a anthu komanso mwayi ndi ulamuliro pakagwilitsidwe ntchito ka katundu komanso phindu lomwe lapezeka pakhomo kapene mmudzi.
  • Kafukufuku kapena kauniwuni wa momwe nkhani za jenda zayendera kapena m’mene zikuyendera ndikupereka tsatanetsatane wa momwe zinthu zikuyenera kukhalira.
  • Zonse zomwe zayenda bwino ndi zomwe zavuta zimadziwika panthawi yi.

DZIWANI IZI: jenda ndi chibadidwe ndizosiyana. Jenda imasintha chitsanzo mwamuna akhoza kukolola chimanga chimodzimodzi mkazi. Chibadidwe sichisintha monga mkazi akhoza kuyamwitsa mwana koma mwamuna sangathe zitavute maka.

 

2.0 KUSIYANITSA JENDA NDI CHIBADIDWE NGATI MUNTHU WA MMUNA KAPENA WA MKAZI

MWININYUMBA AOMBELA MUNTHU

Usiku wina mwini nyumba anamva kuwuwa kwa agalu panja ndipo atatsegula zenela la kuchipinda anaona munthu akuyenda monyang’ama (tip-toeing) kuchokela pa geti la mpanda wawo. Nthawi yomweyo mwini nyumba uja anatenga mfuti ndikuombela munthu uja ndipo anafera pomwepo. Atayang’anitsitsa munthu wakufa uja, mwini nyumba uja analira mokweza “mayo ndapha mwana wanga’’ Nthawi yomweyo anatenga mfuti ija ndikuziombela mkufera pomwepo. Mmene zimachitika izi, mwanayo amachokela kokaona nzake atathawa mnyumbamo osatsanzika.

Kambilanani izi:

Talingalilani kuti inuyo munali mlonda wapakhomopo ndipo a polisi akufuna kulemba umboni wa zomwe zinachitika, mukhoza kufotokoza bwanji za zomwe zinachitika? Mwachitsanzo:

  • Wakupha nzake anali ndi ndani?
  • Kodi wakuphayu anali wamwamuna kapena wamkazi?
  • Kodi waphedwayu anali wamwamuna kapena wamkazi?
  • Kodi chinamupangitsa wakuphayu kuombela winayu ndi chani?  

 

Tsopano funsani anthu awiri aonjezele pa zomwe oyamba uja wafotokoza. [khalani tchelu mmene anthuwa azifotokozela za anthu awiriwa. Ambiri afotokoza kuti okupha ndi ophedwa ndi amuna (Bambo ndi mwana wake wamwamuna)

Kuomba mkota:

  • Mukugwilizana ndi zomwe afotokoza anthuwa? Ngati akugwilizana nazo funsani izi:
  1. Chimene chatipangitsa kuti tiganize kuti anthu awiriwa anali amuna ndi chani? Lembani zomwe zikuyankhidwa.
  2. Maganizo anu ndi otani pa anthu awiri amenewa? Ndi mmene zimakhalila nthawi zonse?

Malizani ndikunena kuti, awa anali mayeso chabe kuti tione mmene anthu timaganizila za makhalidwe amuna komanso akazi mmidzi mwathu. Maganizo amenewa amachokera mu zomwe tadutsamo, malingaliro, zidziwitso komanso kudziwa kwa zinthu zina ndi zina. Tsindikani zakufunika kumvetsetsa mmene maganizidwe amunthu komanso komwe tikuchokela kumathandizila mmene tiganizila nkhani za jenda komanso chibadwidwe mmoyo wathu wa tsiku ndi tsiku. Maphunziro awa atithandiza kumvetsetsa nkhani za jenda komanso mmene nkhani zimenezi zimakhudzila chitukuko kuphatikizapo kayendetsedwe ka magulu ndi makomo athu.

JENDA NDI CHITUKUKO CHA ULIMI KUDZELA MUMASUKULU A PAMUNDA (FARMER FILED SCHOOL), MA BANK MNKHONDE (S4T) NDI MAGULU OPEZA MISIKA YODALILIKA (CPG/CV) ZIMAYENERA KUYENDERA LIMODZI. Kuyendera pamodzi kwa maphunziro a jenda ndi maphunziro apamunda, ma bank mnkhonde ndi ma CPG/CV kutha kuthandizira kuti chitukuko chipite patsogolo mokomera aliyense; abambo, amai, anyamata, atsikana ndi anthu omwe ali ndi ulumali osiyanasiyana; pakhomo, pagulu, ndi m’midzi yathu. Pakali pano ma gulu ambiri a project ya THRIVE akuwoneka kuti mamembala ambiri ndi amayi. Ngakhale izi ziri chonchi, maudindo autsogoleri ambiri amatengedwa ndi abambo komanso abambo ndi amene amatengapo mbali kwambiri pa nkhani yoyankhula pazochitika mmaguluwa.

SEWERO LA JENDA NDI CHIBADIDWE

Ndondomeko (Statement)

Chibadidwe

Jenda

1

Amuna ndiye eni ake malo olima

 

 *

2

Azimayi amaphika

 

 *

3

Azimayi amayamwitsa ana

 *

 

4

Amuna ndiwo ayenela kupeleka chakudya pakhomo

 

 *

5

Amuna amatha masamu pamene akazi amatha zoimbaimba

 

 *

6

Amayi amatenga mimba

 *

 

7

Amayi asamalankhule pagulu

 

 *

8

Amuna amapanga zisankho za ndondomeko za pa banja komanso kuchuluka kwa ana omwe angakhale nawo

 

 *