3.0 MMENE ZA JENDA ZIMAYENDERA PAKATI PATHU (SOCIAL CONSTRUCTION OF GENDER)
Jenda imapangidwa kudzela mu ndondomeko komanso magulu amene anthu amagwilitsa ntchito pakupeleka ntchito, maudindo komanso zomwe tikuyembekezela kwa munthu chifukwa ndi wamwamuna kapena wamkazi mu chikhalidwe chathu. Ndi ndondomeko imene nzeru, zikhalidwe komanso maupangili amaphunzilidwa komanso kuvomelezedwa mmudzi. Imapititsa patsogolo kuphunzila kwa munthu pa zinthu zimene mudzi umaona ngati zabwino kapena zoipa. Ndipo maphunziro amenewa amapitilila kuchokera m’badwo wina kupita m’badwo winanso.
MAGULU NDI NDONDOMEKO ZOMWE ZIMAPANGA JENDA MADERA OMWE TIKUKHALA
Banja lomwe tikuchokela ndi dera lomwe tikukhala
Banja ndi dera lomwe tikuchokela limapeleka udindo komanso mphamvu kwa abambo, amayi, anyamata ndi atsikana, mwachitsanzo:
- Kukondeledwa kwa mwana kutengela ndi chabadidwe chake (kaya wammuna kapena wamkazi)
- Pamene mwana wabadwa ntchito zake zimadziwikilatu potengela mphatso zomwe akupatsidwa monga mtolo wankhuni kwa mwana wamkazi kapena mkondo kwa mwana wammuna
- Ndondomeko yosiilidwa chuma pamene makolo amwalira imapita kwa mwana kutengela ndi chibadwidwe chake
- Ana ena malingana ndichibadwidwe chawo amatengedwa kuti ndi alendo pakhomo
Sukulu ndi Maphunziro
Maphunziro amakhazikitsa maganizidwe komanso zikhulupililo zina zomwe ma banja/makomo komanso madera anadzala kale mwa anthu. Zina mwa mfundo zina zomwe masukulu amakhazikitsila nkhani za jenda ndi:
- Aphunzitsi ndi zitsanzo zabwino komwe ana amatenga nzeru komanso malangizo.
- Aphunzitsi ambiri amuna ndi amene amaphunzitsa ma phunziro a sayansi
- Mkulu wa sukulu zambiri amakhala amuna
Zipembedzo
- Chipembedzo chimapititsa patsogolo kusiyana kumene kulipo pakati pa amayi ndi abambo.
- Malemba ena omwe amagwilitsidwa ntchito amathandizila kupeleka ulamuliro ochuluka omwe uli ndi abambo.
- Ma udindo ambiri muzipembedzo amapelekedwa kwa azibambo ngakhale amene amapita kwambiri kutchalitchi ndi amayi.
- Mipingo ina azimayi saloledwa kulalilkila
ZIKHALIDWE ZOSIYANASIYANA
Nthano, nkhani, nyimbo komanso miyambi ina imapitsitsa patsogolo kusiyana komwe kulipo pakati pa akazi ndi amuna mmadera omwe tikuchokela.
Mwachitsanzo Nyimbo ngati: Kapilire unka iweko, or Wamkulu ndani m’banja.
Nthawi zambiri mkati mwa nyimbo zimenezi mumakhala uthenga komanso matanthauzo osiyanasiyana. Nyimbo zimenezi zimakhazikika komanso kuvomelezedwa ndi anthu komanso dera lomwe akuchokela posatengela zotsatila zomwe zingabwele ndi mauthenga amenewa.
4.0 OMWE AMAKHUDZIDWA NDI NKHANI ZA JENDA
Munthu aliyense amakhudzidwa ndi nkhani za jenda kuchokela nthawi yomwe iye anabadwa. Pamene mwana afika zaka zisanu zakubadwa amakhala wadziwa komanso kuvomeleza za ntchito komanso udindo omwe umapelekedwa kwa iye.
- Mmene atsikana amakhudzidwila ndi nkhani za jenda
- Kusalidwa komwe kumadza chifukwa cha zikhulupililo zosiyanasiyana zimapeleka chiphinjo kwa mtsikana kuti akwanilitse ena mwa maufulu ake monga ufulu kumaphunziro, chitetezo, umoyo wabwino komanso ufulu otengapo mbali.
- Kusalidwa kwa atsikana nthawi zambiri kumayamba ngakhale asanabadwe ndipo kumapitilira pamene akukula mpaka unamwali wawo.
4.2 Mmene anyamata amakhudzidwila ndi nkhani za jenda
- Nthawi zambiri anyamata amapindula ndizikhulupililo zomwe zimapeleka umoyo wabwino komanso kukula kwabwino.
- Anyamata amalimbikitsidwa kuti asamaonetse kukhudzika pa zinthu zina, akhale alusa komanso azitha kuthetsa mavuto omwe akukumana nawo pawokha posafunsila thandizo kwa ena.
- Anyamata omwe anakulila mmakomo kapena madera omwe amachitilidwa nkhanza, amadzakhala ankhanza kwa amayi ndi ana mtsogolo.
4.3 Mmene Amayi amakhudzidwila ndi nkhani za jenda
- Zikhalidwe zambiri zimapangitsa kuti azimayi azisalidwa mu zambiri. Kusalidwaku kumachokela pomwe ali mtsikana mpaka moyo wawo onse.
- Amayi ambiri akukumana ndi nkhaza zosiyanasiyana zomwe zimawapangitsa kusatenga nawo mbali muzitukuko zosiyanasiyana.
- Amayi ndi atsikana amagwila ntchito zambiri zosamalilila pakhomo komanso kusamalila anthu.
4.4 Mmene Abambo amakhudzidwila ndi nkhani za jenda
- Abambo ali ndi mphamvu zambiri muzachuma ngakhale chikhalidwe komanso amapindula ndizikhulupililo zomwe zimapeleka umoyo wabwino komanso kutukuka mwachangu.
- Azibambo ambiri amapangila nkhanza ana ndi amayi komanso ndi omwe amazipha kwambiri akakumana ndi mavuto chifukwa cha momwe anakulila kuti mwamuna asamaonetse kufooka pakufotokoza mavuto omwe akukukamana nawo.