Module Articles

Maphunziro a GESI

Maphunziro a GESI

JENDA MU PROJECT YA THRIVE

5.0 JENDA MU PROJECT YA THRIVE

NSANAMILA ZISANU ZA JENDA MU THRIVE

  • ACCESS-mwayi otha kugwilitsa ntchito katundu ndi phindu, kukhala ndi ulamuliro, kukhala ndi katundu etc.
  • Participation - kutenga nawo mbali mu zochitika zosiyanasiyana zokhuzana ndi chitukuko chamu dela           
  • Decision-making - Kupanga nawo ziganizo mosaopsyezedwa kapena moumulizidwa pa iwe wekha, pabanja, mmudzi etc
  • Systems (Kupezeka kwa ma dongosolo osiyanasiyana amene amapititsa patsogolo umodzi komanso kuona zofuna za magulu osiyanasiyana a anthu monga a ulumali, amayi ndi achinyamata komanso kupeleka mpata/malo omwe magulu onse a anthu angatenge nawo mbali)
  • Well-being (Moyo wabwino- munthu amve kufunika, kutetezedwa, kuzidalira, ukhale ndi umoyo wabwino mmaganizidwe, mu uzimu etc)      

 

6.0 KUFUNIKA KWA JENDA MU PULOJEKITI YA THRIVE

Kuika nkhani zokhudza jenda mu pulojekiti ya thrive ndikofunika kwambiri chifukwa:

  • Kumathandiza kuti alimi akolole komanso kugulitsa zochuluka zomwe zimapangitsa kuti agule ma sheya ochuluka ku magulu a kusunga ndi kubwereketsa kuthandizila kukweza chuma cha khomo lawo
  • Kumathandiza kuti magulu onse a anthu (abambo, amayi, achinyamata ndi olumala atengekepo mbali muzochitika za mupulojekiti popeleka maganizo momasuka zimene zimapititsa chitukuko patsogolo
  • Kumapeleka chiyembekezo ndi chilimbikitso komanso mphamvu kwa magulu onse a anthu mu ulimi ndi ntchito zina zosiyanasiyana
  • Magulu omwe amaikamo nkhani za jenda ntchito zokhudza ulimi kapena misika zimamalizika mwachangu komanso mu nthawi yake

 

7.0 MMENE TINGAYIKILE NKHANI ZA JENDA MU PULOJEKITI YA THRIVE

Pali ndondomeko zinayi zomwe tingatsate kuti nkhani za jenda ziphatikizidwe mu ntchito zomwe tikugwila mu project ya THRIVE

STEP 1 Kupeza mavuto okhudza jenda (Identification)

  • Kupeza mavuto okhudza jenda kumafunika kupanga kafukufuka pogwilitsa ntchito njira zosiyanasiyana zomwe mudzi onse umatengapo mbali
  • Abambo, amayi, anyamata, atsikana ndi anthu olumala amafunika kutenga nawo mbali mukafukufuku umenewu
  • Mavuto okhudza jenda omwe apezeka popanga kafukufuku amafunika kulembedwa komanso kuikidwa mu ndandanda malingana ndikukula komanso kufunikila kothana ndi vutolo
  • Pulojekiti iliyonse imafunika kuonetsa mavuto a jenda omwe akhale akuthana nawo mu nthawi ya pulojekitiyo

STEP 2 Kuvomeleza mavuto a jenda omwe apezeka (Internalization)

  • Mavuto okhudza jenda akapezeka komanso kuikidwa mundandanda magulu onse a anthu mudzimo akufunika kuvomeleza komanso kukhudzika ndi mavuto omwe apezekawo.
  • Njira zosiyanasiyana monga maselewelo (drama), kukambilana magulu (focus group discussions) ndi zina zotero zimagwilitsidwa ntchito kuti anthu avomeleze komanso kukhudzika ndi mavuto omwe apezeka

STEP 3 Kuika ndondomeko zothetsela mavuto a jenda (Integration)

  • Mavuto a jenda omwe apezeka pakufunika kuika ndondomeko komanso ntchito zomwe magulu onse a anthu adzagwile pothana ndi mavutowo mu nthawi yomwe pulojekiti ikuyamba kufikila kumathelo a pulojekitiyo.
  • Mavuto ena omwe pulojekiti siingakwanitse kuthana nawo amayenekela kupelekedwa kwa mabungwe omwe ali ndikuthekela kothandiza kuthana ndi mavutowo

STEP 4 Kupititsa ntchito za jenda patsogolo (Institutionalization)

  • Ndondomeko zothetsela mavuto a jenda zikaikidwa pakufunika kupititsa ntchito za jenda patsogolo monga kusankha komiti yomwe idziyendetsa komanso kuona nkhani zokhudza jenda mmudzi

 

8.0 KUZIUNIKA TOKHA NGATI GULU KAPENA BANJA

 

 

 

9. KODI MAGULU MONGA: MASUKULU A ALIMI (Farmer Filed School), MABANK MKHONDE(S4T) NDI MAGULU OLIMILA NDI KUGULITSILA MALONDA PAMODZI (CPG/CV) ANGAMAUNIKILE NKHANI ZA  JENDA MU PULOJEKITI YA THRIVE

  1. Magulu amathandiza kupititsa patsogolo ntchito za ulimi ndi malonda komanso kuti alimi apeze ndalama zochuluka kuti athane ndi mavuto a njala kumanso kunyentchera pa khomo, mmudzi ngakhalenso mu dziko
  2. Pamene alimi akukolora mbeu komanso kusunga ziweto zochuluka nkhani za malonda zimapita patsogolo. Malonda a mbeu ndi ziweto amathandiza kuti alimi akhale ndi ndalama zotha kugulira zofunika pa khomo pawo.
  3. Magulu amathandiza kuti amayi athe kumaphunzira njira za makono zogwilira ntchito pamodzi ndi abambo
  4. Magulu amapereka mwayi kwa aliyense (abambo, amayi, anyamata komanso anthu aulumali) kukhala atsogoleri
  5. Magulu amapereka mwayi ku magulu onse a anthu abambo, amayi, anyamata komanso anthu aulumali) kumasuka kupereka maganizo awo kuti gulu lipitilire kugwira bwino ntchito

 

10. MAFUNSO OYENERA KUFUNSA KUTI TIDZIWE NGATI NKHANI ZAJENDA TIKUCHITA BWINO

  1. Kodi membala aliyense akutha kupereka maganizo ake momasuka pa ziganizo ndi zisankho zomwe gulu likupanga?
  2. Kodi ma lipoti a GESI akumakhala okhudza gulu lonse? Kodi ma lipotiwa akutha kuonetsa bwino lomwe mmene gulu lonse (abambo, amayi, anyamata komanso anthu aulumali) akutengelapo gawo mu pulojekiti
  3. Kodi ntchito za pulojekiti komanso ma pulani a pulojekiti akutha kuonetsa mmene abambo, amayi, anyamata komanso anthu aulumali azitengelapo mbali
  4. Kodi phindu lonse la pulojecti ndilopezekelatu kwa abambo, amayi, anyamata komanso anthu aulumali onse omwe akutengapo mballi.
  5. Kodi ma udindo a utsogoleri, kupanga zisankho komanso ziganizo za gulu zikumagawidwa bwanji pakati pa abambo, amayi, anyamata komanso anthu aulumali.