Module Articles

Maphunziro Okonzekera Ngozi Zogwa Mwadzidzidzi Ndi Covaca

Maphunziro Okonzekera Ngozi Zogwa Mwadzidzidzi Ndi Covaca

COVACA (Chichewa Version)

(COMMUNITY OWNED CAPACITY AND VULNERABILITY ASSESSMENT)

KAFUKUFUKU WA M’DERA WOPANGIDWA NDI ENI DERA POFUFUZA ZA KUTHEKERA NDI UMBALAMBANDA OMWE UKUPEZEKA M’DERA

CHINDUNJI

  • Eni  mudzi ali ndi kuthekera kolimbana ndi umbalambanda omwe ukupezeka mudera mwawo
  • Kafukufuku ameneyi amapangidwa ndi eni ake a chitukuko/  kuunikilana ndi kuphunzitsana za zinthu zozindikilitsa/zosonyeza kapena zolosela ngozi zogwa mwadzidzidzi//

NJIRA YA COVACA IMASIYANA BWANJI NDI NJRA ZINA

  1. Kugwiritsa ntchito nzeru zomwe eni mumudzi ali nazo m’mudzi mu ndondomeko yonse ya kuthana ndi ngodzi zogwa mwadzidzi – popanda kuikamo nzeru za obwera
  2. Kafukufuku uyu amapangidwa ndi eni ake amumudzi
  3. Cholinga cha kafukufuku uwu ndi wolimbikitsa eni ake a mumudzi kuti apeze zomwe angapange pothana ndi ngodzi zogwamwadzidzi pogwiritsa ntchito kuthekera komwe ali nako, mosadalira othandiza ena. 
  4. Zotuluka mu kafukufukuuwu ndi zothandiza eni nzika osati akunja

ZOLINGA ZA COVACA

  1. kupanga kafukufuku wa umbalambanda  ndi kuthekera kuti apange chisankho chabwino pa zochita pozitetezera komanso kupewa
  2. Kupeza zomwe anthu amumudzi  angathe kupanga pogwiritsa ntchito kuthekera komwe ali nako
  3. Kupeza fundo zokhuzana ndi ziopsyezo, umbalambanda ndi kuthekhera komwe kulipo, njira zochepetsera maululu kuti tithe kuyika dongosolo lazinthu zomwe zingatithandize kupewa ndi kuchepetsa maululu ndiposo kubwezeretsa moyo muchimake

UBWINO WA COVACA

Kugawana Nzeru ndi Luso

  • Zimathandiza eni nzika kugawana fundo ndi nzeru zoti zitha kuwathandiza kupeza njira zochepetsera ululu komaso kulimbikitsa upangiri waku khazikitsa ntchito zokhudzana ndi ngodzi zogwa mwadzidzidzi

Kupeleka UMWINI

  • Njira iyi imapangitsa nzika kukhala ozidalira komanso kuzindikira kufunikira kwao pa chitukuko chili chonse chochitika mdera lawo kuphatikisirapo kulimbana ndi ngodzi zogwa mwadzidzidzi
  • Imapangitsanso kuti nzika isamakhale yozidelera pa nkhani/zinthu zochitika mudera lawo
  • Siifuna mathandizo ena apadera kapena ochoka kwina koma mumudzi mwao mommo

 

CHILIMBIKITSO POGWIRITSA NTCHITO NJIRA YA COVACA

  • Imalemekeza nzeru za m’mudzi, kutengapo mbali komanso umwini wa fundo zotuluka mukafukufukuwu
  • Kumapanga aliyense akhale wosangalala ingakhale munthawi yamabvuto

kuthekera komwe tilinako mumudzi mwathu kungathe kupulumutsa moyo – tisadikire mathandizo obwera ndipo tigwiritse ntchito moyenera kuthekera komwe tili nako mudera mwathu

DONGOSOLO LA KAKONZEDWE KA NDONDOMEKO YA KUMUZDI YA NTCHITO ZOKONZEKERA NGOZI ZOGWA MWADZIDZIDZI (CDPP)

Mawu Oyamba

  • CDPP ndi ndondomeko/dongosolo la ntchito lomwe eni nzika amapanga ndi kukhala nayo umwini kukati ngozi yogwa mwadzidzidzi yawachitikira.
  • CDPP imalongosola mwatsatane tsatane zonse zoyenela kuchita ngati ngozi yogwa mwadzidzidzi itachitike monga kukonzekera, kuchitapo kanthu, kuchepetsa ndi kubwezeretsa m’chimake (DRM CYCLE) ndipo izi zimatengela kafukufuku yemwe eni nzika anachita pa ziopsyezo, umbalamabnda, kuthekhera kwao ndi zinthu zolosera ngozi (HVC&EWS ANALYSIS)
  • CDPP imakonzedwa ndikusungidwa muchilankhulo cha ENI NZIKA. Ofuna kugwilitsa ntchito CDPP imeneyi ayenela kupeza chilolezo kuchoka kwa ENI NZIKA.
  • CDPP ndi pulani ya moyo ndipo iyenela kuunikilidwa ndi ndikukonzedwanso nthawi ndi nthawi.

Cholinga - Purpose/expected outcome

  • Kukonza dongosolo la ntchito zoyenela kutsata ngozi yogwa mwadzidzidzi itati yachitika.

MFUNDO ZOYENELA KUTSATA POKONZA CDPP

  • CDPP ndi ya anthu a kumudzi/ imalelembedwa m’chilankhulo cha eni dela ndi eni dela/ CDPP siya WORLD VISION AYI//
  • CDPP iyenela kugwilizana ndi mfundo/mapulani/ntchito za Boma/Mabungwe omwe akugwila nawo ntchito m’deralo eg Annual Operational Plan/ DDP//
  • CDPP iyenela kuthandizila kukonza mfundo/mapulani/ntchito za Boma komanso Mabungwe zokudzana ndi ngozi zogwa mwadzidzidzi/
  • Iyenela kukhala ya dela lalikuluko, kuphatikiza ngakhale midzi ingapo//
  • Eni nzika ayenela kutenga gawo lalilkulu potsogolera ntchito yo konza CDPP/

CDPP njamoyo ndipo iyenela kuunikilidwa ndikukonzedwanso pannthawi zokazikiaka (pakadutsa miyezi 6 ndinso pa chaka

NDONDOMEKO YAKAKONZEDWE KA CDPP YA CHIDULE

  • Mitu yofunikila kuika mu CDPP ndi iyi:
  • Ngozi Zomwe zingachitike
  • Madera omwe anga khudzidwe
  • Mndanda wa anthu, mabanja ndi zinthu zomwe zingakhudzidwe
  • Njira zomwe zili m’malo kuchepetsa ngoziyi
  • Anthu omwe awongolele/kutsogolera ntchito
  • Ndondomeko yobwezeretsa m’chimake pomwe ngozi yapita
  • Kuchuluka kwa ndalama zofunika pothandizira pomwe ngozi yachitika