Module Articles

Maphunziro Okonzekera Ngozi Zogwa Mwadzidzidzi Ndi Covaca

Maphunziro Okonzekera Ngozi Zogwa Mwadzidzidzi Ndi Covaca

Kulimbana Ndi Ngozi Zogwa Mwadzidzidzi Nyengo Zonse

KUKONZEKERA NGOZI ISANACHITIKE (PRE-DISASTER)  

Ntchito/ndondomeko zimene tingapangiretu/kukhazikitsa kuti tisadzasowe chochita chiopsezo chitachitika.

  • Kuzindikiritsidwa ndi kulimbikitsa kuthekera komwe tirinako mothandizana ndi:
    • Boma/ Mabungwe omwe ali ndi upangiri wochitapo kanthu  ndi kubwenzeletsa/Madera athu ndi Anthu//
  • Kuti tikwanitse:
    • Kuzindikira/ Kuchitapo kanthu/ ndi kukozanso zimene zingabwere kamba ka ziopsezo zomwe tili nazo.

Zolinga Zakukonzekera

  • Kupititsa patsogolo ndondomeko/ukadaulo wabwino pathawi imene tikuchitapo kanthu pothandiza mabanja/ madera/ maboma komanso dziko lomwe lakhudzidwa ndi mavuto// Zina mwa izi ndi:
  • Kukhazikitsa ndi kuyeserera ndondomeko/zida zotichenjezeratu mavuto asadachitike

Maphunziro awanthu ogwira ntchito komanso anthu amene ali pachiopsezo// Kuphunzitsa magulu amene adzathe kuthandiza athu ngati votu lagwa/ Kukhazikitsa ndondomeko/mapulani omwe adzatithandizire thawi yamavuto ikapita//

  • Kulimbitsa anthu am’dera lathu kuti azitha kukonzekera pawokha pokhazikitsa ntchito zomwe iwo akhoza kuzigwira posafuna chithandizo chochokera kwina//
  • Kukhazikitsa nthito zofunikira pothana ndi kukhala pachiopsezo tsiku ndi tsiku ndi cholinga choti tidzathe kuchitapo kanthu ngati vuto latipeza//

(njira) Zoyenera Kutsata Pokonzekera ZIOPSYEZO kanena NGOZI zogwa mwadzidzi:

  • Kuchita kafukufuku wa chiopsezo/ pachiopsezo and paumbalambanda//
  • Ndondomeko zabwino zochitapo kanthu,
  • Mapulani akukonzekera,
  • Kulumikizana pogwira ntchito,
  • Kusamala malekodi
  • Njira/ndondomeko zotichenjezeratu
  • Kutolerera/kusonkhetsa katundu/zofunikira
  • Kuphunzitsa anthu
  • Anthu am’mudzi akhale okonzekera pawokha

Kuchitapo Kanthu;

  • Kuthandizira panthawi imene ngozi yangochitika komanso munthawi yangozi
  • Kuchitapo kanthu kukuyenera kuchitika motsata zofuna zaanthu okhudzidwa osati mongoganiza.

  • Ndondomeko yakuchitapo kanthu ya IRC imayang’ana pangodya khumi:
  1. Zofuna zaanthu zimaikidwa patsogolo.
  2. Chithandizo chimaperekedwe posayang’ana mtundu, chipembedzo komanso dziko lochokera// Ndipo thandizo limaperekedwa poyang’ana zosowa za anthu okhudzidwa basi//
  3. Thandizo lisagwiritsidwe ntchito pofuna kupitisa patsogolo zofuna za ndale kapena mpingo//
  4. Sitikuyenera kugwira ntchito popititsa patsogolo mfundo zaboma zomwe zili zosayenera kudziko//
  5. Tilemekeze chipembedzo ndi zikhulupiriro za okhudzidwa//
  6. Tichitepo kathu popititsa patsogolo kuthekera komwe anthu alinako//
  7. Tipeze njira zogwirira ntchito pamodzi ndianthu okhudzidwa//
  8. Chithandizo chichepetse Chiophyezo/ komanso anthu anthe kukhutira nacho//
  9. Tichite chilungamo ndi anthu ofuna thandizo komanso kwa omwe akutithandiza//
  10. M’malekodi athu ngakhale pofalitsa nkhani/ tiwalemekeze anthu okhudzidwa ndi ulemu wawo/ osati ngati anthu opempha//