Kuchenjeza pomwe ngozi isanachitike/ ndi mbali yofunikila kwambiri pa nctchito yochepetsa ngozi zochitika mwadzidzidzi// Izi zimateteza moyo/ ndi kuchepetsa kuwononga chuma komanso katundu//, kuti izi ziyende bwino/ ndondomekoyi iyenela kuika eni okhudzidwa patsogolo ncholinga chakuti/ atenge nawo gawo/kuphunzitsa ndi kuunikila anthu za kukhala pa chiopsyezo, komanso kumwaza machenjenzo ndi kuonetestsa kuti anthu ali okonzeka nthawi zonse
Cholinga
Kumvetsetsa, kugawana nzeru ndi luso pankhani ya zizindikilo/zolosela ziopsyezo/ngozi zosiya-siyana zomwe zimakhudza antuhu ku midzi
Zoinga mwachindunji
- Kumvetsetsa tanthauzo/ ngondya zinai zazindikilo/zolosela ziopsyezo/ngozi zosiya-siyana
- Kudziwa mitundu ya zizindikilo/zolosela ziopsyezo/ngozi zosiya-siyana
- Kukambila zizindikilo/zolosela ziopsyezo/ngozi zosiya-siyana zomwe anthu akumudzi akuzidziwa ndi mmene amazigwiritsira ntchito
A. Thanthauzo la “Warning” ndi “Sign” (chezengezo komanso zizindikilo)
- Ndi chinthu chomwe chimachitika ndi kulosera kuti kutha kukhala chiopsyezo/ngozi.
- Chinthuci chimadziwitsa anthu kuti kutha kukhala “DANGER” VUTO kapena CHINACHAKE CHOSAKHALA BWINO.
B. Nanga “Early Warning System” ndi chiyani?
- Early Warning System (EWS) ndikuthekhera komwe kumafunika/ kuti anthu apeze/ ndi kufalitsa uthenga wa tanthauzo panthawi yake/ kuti anthu omwe ali pa chipoysezo cha ngozi/ athe ndikuchitapo kanthu moyenelera/ ngoziyo isadachitike/ ndi cholinga choti achepetse kuonongeka kwa katundu komanso kutaya moyo/ chuma ndi katundu//
- Anthu omwe ali pachiopsyezo AYENELA kutengapo GAWO LALIKULU