Module Articles

Nthochi

Nthochi

Mitundu

Mitundu (Chichewa)

MAWU OYAMBIRIRA

Nthochi ndi mbewu yofunika m’dziko muno. Mbewuyi ndiyodalirikanso mmayiko a ku Africa komanso kugulitsa kuti apeze phindu. Imagwitsidwa ntchito ndi alimi ang’onoang’ono ngati chakudya pakhomo. Nthochi zikuthandiza kwambiri kuthetsa kuchepa kwa zakudya m’dziko. Nthochizi zikulimidwa kwambiri masiku ano chifukwa anthu azindikira kuti mbewuyi imakula kumadera onse malingana ndi malo.

Cholinga chachikulu ndi Kuwonjezela ukadaulo ndi nzeru pakati pa alimi ang’onoang’ono amene akulima nthochi kuti apezeke zokolola zambiri.

Pomaliza pa phunzilori alimi akuyenera kudziwa:

  • Njira zabwino zothandizira ulimi wa Nthochi.
  • Momwe angatetezele ndi kusamalira Nthochi ku tizirombo ndi matenda.
  • Nzeru zothandizila kusintha ulimi wa nthochi kukhala waphindu.
  • Nzeru za kasamalidwe ka nthochi zokololedwa.

MITUNDU YA NTHOCHI

Ina mwa mitundu yanthochi ndi iyi:

  • Kabuthu, Williams ndi Mulanje. Kabuthu amatha kukolola kufika   60,000 kg hekitala iliyonse ngati miyambo yabwino yatsatidwa.
  • Mitundu ina iwiriyi mlimi amakolola kawiri pachaka

Nyengo zoyenera

  • Nthochi imasangalala padothi lakuya limene lili la manyowa okwanira.
  • Ulimi wa nthochi umakhala bwino kumene mvula imagwa kuposela 1200mm ndi kumene mulingo wa mchele pakati pa 5.6 ndi 6.5.