Nthochi
Matenda Ndi Tizilombo
- Nyongolotsi: zimaononga mizu ndipo mizu imaola.
- Nankafumbwe: Tizirombo timakumba mabowo akuda mu mizu ya mbewu ya nthochi. Zilombozi zimapezeka kwambiri m’malo osapalilidwa bwino.
Kupewa tizirombo:
- Kubzala ana anthochi aukhondo.
- Palirani minda molongosoka.
- Bzala mitundu ya nthochi yopilila.
- Pamene mbewu yakhudzidwa kwambiri ichotsedwe ndipo pamalopo pabzalidwe mbeu yina.
Black Sigatoka
- Matenda awa amakhudza masamba ndi nthochi. Amayamba ndi mizele yakuda imene imatalika ndi nthawi ndikusintha mtundu kukhala a mtundu wa ngati matope.
- Matenda awa amapezeka kwambiri nthawi ya mvula ndipo matenda akapitilira mbewu zimafa
- Bzalani mbewu zopilira kumatendawa komanso mwakasinthasintha.
Nthomba
- Matendawa amgwira masamba ndipo amapangitsa masambawo kukhala amadonthomadontho ndikunduka a chikasu.
- Bzalani mbewu zopilira kumatendawa komanso mwakasinthasintha.
Fusarium Wilt
- Imatseka mmene mumadusa madzi mkati mwa mtengo wanthochi.
- Amaononga mizu ndi tsinde lanthochi.
- Matendawa amagwira kwambiri mitundu yanthochi ya magombo ndi zambia.
- Amapezeka kwambiri mu dothi la makande.
Khate(athracnose)
- Matendawa amapangitsa makoko anthochi kukhala a madonthomadontho ndipo akapitilira nthochizo zimaola.
- Otchani zipatso zonse zimene zagwidwa ndi matendawa.
- Zokolola zimene sizinagwidwe ndi matendawa zisungwidwe ku malo osungila zokolola a ukhondo.
- Onetsetsani kuti nthochi zosupuka zisapite malo ena.
Cigar-end rot
- Matendawa amagwira nsonga za nthochi ndipo nthendayi ikapitilira chipatso chonse chimada.
- Pewani matendawa pochotsa timaluwa ku nsonga kwa nthochi zikakhwima.
Kuwola kwa mizu
- Matendawa amaoletsa mizu ya mtengo wa nthochi ndipo pamaoneka khungu loyera.
- Dulani mitengo yosafunika yonse zaka ziwiri isanafike nthawi yobzala nthochi.
Chisaka
- Matendawa amagwila mitundu yonse ya nthochi.
- Amafalisidwa pamene zobzalila mbewu zikusunthidwasunthidwa.
- Amapangisa mbewu kukula mopinimbira ndipo masamba ake amakhala ofota komanso okhakhala.
- Imabeleka ana ambiri kuposa m’mene mbewu yopanda matendawa imabelekera.
- Bzalani mbewu yaukhondo ndi yopanda matenda.
- Zulani ndikutentha mbewu zogwidwa ndi matendawa.