Nthochi
Kasamlidwe ka mbeu
- Thilani manyowa munthaka kuti zokolola zichuluke.
- Phatikizani manyowa osachepera 10kg pamene mukubzala nyengo ya mvula.
- Thilani feteleza wa CAN, Single superphosphate ndi 175g Muriate of potash, 75g Urea, 200g 23:21:0+4S ndi175g Muriate Potash podzala paliponse kumayambiliro kwa nyengo ya mvula.
- Mwazani feteleza pa malo podzala ponse ndikuzaphatikiza ndi nthaka ili pamenepo.
- Palirani munda mosamala udzu ukangomera pogwiritsa ntchito makasu kapena gwiritsani ntchito mankhwala opha udzu.
- Patulirani nthochi posiya imodzi paphando.
- Onetsetsani kuti ana a nthochi alipo atatu pa malo odzala.
- Chotsani masamba ndi mabewu zakufa ndikugwilitsidwa ntchito ngati zophimbila.
- Thilirani madzi ambiri nthawi imene mbewu ikupanga maluwa.
- Thilani madzi tsiku lirilonse mmadela otentha pamene dothi lapamwamba lawuma.
- Thilirani pafupipafupi koma osapitilila muyeso chifukwa nthochi zimaola.