- Mbewu ya nthochi imakhwima malingana ndi mtundu wake
- Dulani mkoko wanthochi ndi mpeni wakuthwa pamene nthochi yakhwima.
- Onetsetsani kuti phava lanthochi litsale kutsinde losachepera 15cm kuti linyamulike bwino.
- Nthochi zokololedwazo zikasungidwe m’malo amdima ozizilira bwino.
- Zokolora zikutidwe ndi masamba a nthochi ouma kuti zisaonongeke.
Chidziwitso: Tsukani nthochi ndikuziyanika, chotsani nthochi zonse zoonongeka. Nthochi zonse zipite ku misika zidakali zosapsa kuwopa kuti zingaonongeke.