Module Articles

Nthochi

Nthochi

Kukolola

  • Mbewu ya nthochi imakhwima malingana ndi mtundu wake
  • Dulani mkoko wanthochi ndi mpeni wakuthwa pamene nthochi yakhwima.
  • Onetsetsani kuti phava lanthochi litsale kutsinde losachepera 15cm kuti linyamulike bwino.
  • Nthochi zokololedwazo zikasungidwe m’malo amdima ozizilira bwino.
  • Zokolora zikutidwe ndi masamba a nthochi ouma kuti zisaonongeke.

Chidziwitso: Tsukani nthochi ndikuziyanika, chotsani nthochi zonse zoonongeka. Nthochi zonse zipite ku misika zidakali zosapsa kuwopa kuti zingaonongeke.