Soya ndi mbewu imodzi imene imalimidwa ku Malawi. Musoya muli chakudya chokulitsa, mafuta michere ina yofunikira m’thupi la munthu, ndi kubwezeretsa chonde mnthaka. Cholinga chachikulu ndikupititsa patsogolo luso pakati pa alimi ang’onoang’ono la kalimidwe ka soya
Pakutha paphunziloli mlimi akuyenera:
Kudziwa ndondomeko zabwino za kalimidwe ka soya. Njira zabwino zochepetsera tizilombo komanso matenda ogwira soya. Kudziwa upangili wa kachulukitsidwe ndi kasamalidwe ka soya
Ocepara-4 – maso ake ndi akuluakulu, yoyanga komanso yopilira kumatenda a chiwawu.
Nasoko – maso ake ndi akulu, imayanga pang’ono komanso zokolola zochuluka
Makwacha – maso akuluakulu, yoyanga pang’ono, komanso zokolola zochuluka
Solitaire – yopilira kumatenda a maso chule.
Soprano – yopilira kumatenda a maso a chule, zokolola zochuluka
Tikolore – sifunika inoculant, yopilira kumatenda a maso a chule, imagwidwa ndi matenda a dzimbiri
Serenade – imakula moyanga, maso akulu ndipo imabereka kwambiri
PAN 1867 – maso akuluakulu, imakula moyanga koma yobereka mochepa