Module Articles

Soya

Soya

Kukolola

Kololani soya mmawa mame asanathe kuopetsa kuthetheka kwa soya. Dulani soya ndi chisikilo kuti mizu itsale munthaka. Mizu imathandizira kuonjezera chonde mu nthaka. Ombani pang’onopang’ono poopa kuononga mbewu. Petani soya pochotsa zinyalala komanso mphwemphwa. Sankhani soya moyenera. Chotsani soya wa mitundu ina yemwe anangogwerako.

Kusunga Soya

Sungani soya ouma bwino pamalo abwino ndi aukhondo.