Palirani soya pamene udzu wangomera kumene. Izi zimathandiza kuti udzu usapange njere zimene zingadzamere m’chaka chotsatira. Palirani kapena gwiritsani ntchito mankhwala opha udzu – njirazi zikhoza kugwiritsidwa ntchito iliyonse payokha kapena kuphatikiza. Palirani udzu m’munda wa soya pakatha sabata ziwiri kuchoka tsiku lobzala.
Thirani Fetereza wokulitsa wa 23:21:0+4S olemera 50kg thumba liri lonse pa hekitala imodzi. Thirani feterezayu nthawi imene mukubzala soya. Pangani mikwasa pakati pa mikwasa iwiri ija mwabzala mbewu zanu ndikuwaza fetereza wokwanira 18g mtunda wa mita imodzi. Pewani kuthira fetereza mochedwa, chifukwa soya azikula koma osabereka