Module Articles

Soya

Soya

Matenda Ndi Tizilombo

TIZILOMBO NDI MATENDA

Mbozi – zimadya masamba a soya ndipo zimachepetsa zokolola. Poperani mankhwala.

Chiswe – chimaononga soya kuyambira ongobzalidwa kumene komanso wokhwima makamaka kukakhala ng’amba. Bzalani mbewu mwakasinthasintha.

Matenda a Soya

Dzimbiri 

Matendawa amagwira masamba a soya ndipo kuseli kwatsambalo kumaoneka chikasu choderako pang’ono. Bzalani soya moyambirira kapenanso thirani mankhwala ochepetsa matendawa.

Mandolo akuluakulu 

Amagwira mizu ya soya ndipo amapangitsa kuti soya asakule komanso asabereke bwino. Bzalani mbewu mwa kasinthasintha kuti muchepetse matendawa.

Kachilombo kosaoneka ndi maso kotchedwa virus

 amafala ndi tizilomba touluka, zitheba za soya zimakhala zochepa. Zulani ndikuotcha mbewu zonse zogwidwa ndi matendawa.