Module Articles

ULIMI WA NKHUKU

ULIMI WA NKHUKU

Matenda Ndi Tizilombo

Matenda ofunikira kwambiri ku nkhuku zing'onozing'ono ndi matenda a chideru chifukwa ndiye amapha ambiri komanso kuwonongeka kwachuma pakupanga nkhuku zam'midzi. Monga lamulo la biosafety, musamadye nyama ya nkhuku  (kapena nyama ya chiweto chilichonnse) yomwe ili ndi matenda kapena yofa ndi matenda ndipo nthawi zonse chotsani mbalame zodwala  zonse pagululo ndi kuzisunga pamalo ena apadera.

Pansipa pali ndandanda ya katemera yomwe alimi amatha kutengera.

Msinkhu

Matenda

Katemera ndi kaperekedwe

Masiku 1-3

Newcastle disease


I-2 kudonthezera mmaso

Masiku 7-14

Infectious bursal disease
(Gumboro)

Bursine-2 kuika mmadzi okumwa

Masiku 14-21

Newcastle disease


I-2  kudonthozera mmso

Masiku 14-21

Infectious bursal disease
(Gumboro)

Bursine-2  kuika mmadzi okumwa

Masabat 8-10 weeks, kenako miyezi 3-4

Newcastle disease


I-2 kudonthozera mmaso

Masabat 5-8

Fowl pox

Poxine kubaya pa phiko.