Module Articles

ULIMI WA NKHUKU

ULIMI WA NKHUKU

Mau Otsogolera

Nkhuku ndi mbalame zomwe zili mu gulu la mbalame zoweta, mu gululi mulinso ziweto monga abakha, nkhunda, nkhanga, zinziri ndi zina Zotero. Bukhuli litsindika pa zaulimi wa nkhuku. Ziweto zina za mgulu la mbalame sizikambidwa mu bukhuli.

Mitundu yankhuku.

Ku Malawi kuno kumapezeka mitundu itatu ya nkhuku, mitundu yin di; nkhuku za makolo zomwe zimatchulidwanso kuti nkhuku za makolo zomwe zimapezeka m’midzimu. Mtundu wina wankhuku ndi nkhuku za ‘hybrid’ kapena nkhuku zachizungu, izi ndi nkhuku zomwe zimawetedwa mumafamu akuluakulu ndicholinga chopezapo nyama kapena mazira. Nkhuku zachizungu zimagulitsidwa mumasitolo mmadera aku tauni. Mtundu wina wankhuku omwe umapezeka muno mMalawi ndi nkhuku za Mikolongwe. Izi ndi nkhuku zomwe zimapezeka mmafamu a boma monga Bwemba, Choma komanso Mikolongwe. Nkhuku za Mikolongwe nthawi zambiri zimagawidwa ndi aboma kapena amabungwe.

Nkuku ya chikuda ndi anapiye ake.