Ulimi wa njuchi ndi othandiza kuti alimi apeze phindu lochuluka komanso kupeza chakudya. Ulimiwu umapereka mwayi kwa alimi kuti ayambe buzinesi mdziko muno komanso kumayiko akunja. Ulimi wanjuchi umapereka zinthu zosiyanasiyana monga uchi, phula ndi zina.
Pomaliza pa phuziroli, mlimi akkuyenera kudziwa:
Ndondomeko zoyenera za Ulimi wa njuchi, nzeru pa ulimi wa njuchi kuti phindu lichuluke komanso nzeru za kasamalidwe ka uchi ukakololedwa.
Kukhazikitsa bwino ndi kusamala ming’oma ya njuchi. Kukolola ndi kufinya bwino uchi ndi phula. Kusankha malo oyenera. Kupeza malo oyenera odyetsera. Kudzadzitsa mng’oma yopanda kanthu. Kugwila nchito ndi zipangizo zoyenera. Kupewa phokoso kapena chisokonezo. Kusunga ming’oma mwaukhondo. Kupewa matenda ndi zilombo.
Ming’oma yokhazikika ndi Ming’oma ya nyambo
Kuteteza ming’oma ku dzuwa, poiika pansi pa mtengo. Kuteteza ming’oma ku mphepo, poiyang’anitsa komwe sikudutsa mphepo. Kuteteza ming’oma ku njoka ndi zinyama zina zachilengwedwe. Kuteteza ming’oma ku mvula. Ming’oma ikuyenera kusungidwa malo otalikana 100m ndi komwe kukukhala anthu. Ming’oma itha kupangidwa kuchokera ku zinthu monga matabwa, dothi ndi zina zambiri. Zinthu zitatu zomwe zimagwilitsidwa mu ulimi wa njuchi. Ming’oma yokhazikika. Ming’oma ya nyambo zochotseka.
Sunthani njuchi poziika pa malo pomwe pali maluwa ochuluka, madzi komanso obisika kuopa kuti ingabedwe kapena kuvulaza anthu. Mangani ming’oma mosamala poonetsetsa kuti palibe potulukira kupatula polowera njuchi.
Gwiritsani zinthu monga sera ya njuchi, olanje, mafuta a zinyumwa ndi zina zonukhira, pakani phula panja pa ming’oma pofuna kukopa njuchi. Ming’oma yaying’ono imakopa njuchi zomwe zikufuna kukhala malo amodzi. Njuchi zimayenera kulowa m’ming’oma pazokha koma mlimi atha kukopa njuchi kuti zilowe m’ming’oma.
Onetsetsani kuti mwavala zovala zoziteteza musanayambe kugwira njuchi, ngati zovala zozitetezera palibe, ndizololezedwa kufukiza utsi kapena kupopera madzi kuti njuchi zifooke. Gwedezani gulu la njuchi mu bokosi loyenera kapena dengu. Sunthani gulu la njuchi mwachangu, kuiika mu mng’oma wa tsopano.