Module Articles

Njuchi

Njuchi

Kukolola

Kololani uchi mukaona kuti zisa zisanu ndi zitatu zamatidwa ndi uchi. Uchi umayenera kukololedwa pakatha miyezi 5 kapena 9. Dulani zisa kuthabwa, ndipo ikani mu chidebe choyera ndipo tsekani bwino kuopa kuti njuchi zina zingadye uchi. Njuchi zimadya uchi, siyani zisa zokwanila kuti njuchi zipeze chakudya. Dulani zisa mzidutswa zing’onozing’ono ndipo finyani uchi ndi nsalu yotelera. Finyani uchi ndi sefa ndipo siyani uchi mchidebe kwa masiku atatu mpaka asanu kuti ukhazikike. Ikani uchi wanu mmbabotolo.    

Phula la njuchi

Dulani zisa zopanda kanthu ndikuziika m’mpoto wa madzi, tenthetsani madzi mpaka zisa zisungunuke. Madzi asawile kapena kubwata, pungulani phula lanu ndikuliika mu chidebe chopakidwa sopo, ndipo dikilani kuti phula lanu lizizile, phula likazizila chotsani ndi kulidula momwe mukufunila.