Chotsani zisa zakale mu mng’oma. Siyanitsani uchi ndi chisa, kuopetsa kuti chisa chingalowe mu uchi. perekani zakudya komanso mpata kuti njuchi zidzadze. Gawani gulu la njuchi kumathandiza kuti njuchi zisaunjikike malo amodzi, izi zimachitika pogawa zisa 12 mpaka 15 kupititsa mu mng’oma ina.
Pewani phokoso ndi kuyendayenda, mafuta onukhira ndi zina zonukhilitsa. Fukizani utsi pofoola njuchi kuti zifatse. Pewani kupha njuchi, chikufwa kumakwiyitsa njuchi zina. Potsegula mng’oma fukizani utsi polowera kenako pitani kumbuyo ndipo dikilani mphindi ziwiri kuti mudziwe komwe kuli uchi musanachotse chotsekera pa mng’oma. Osafukiza utsi wambiri, pakuti umatha kununkhisa uchi. Pewani kuwunjikana kwa njuchi.