Module Articles

Njuchi

Njuchi

Matenda Ndi Tizilombo

Mbozi (Galleria mellonella)  -  ndi tamtundu wa bulawuni, ndipo timagwila gulu la njuchi lofooka chifukwa chosadya mokwanira. Pewani tizilombo poonetsetsa kuti podyetsera bwino njuchi zathu. Patsani sugar nthawi yachilala.

Kafadala (Aethina tumida) - amaononga komaso kudya zakudya za njuchi. pewani poonetsetsa kuti polowela njuchi pasapitilire 1 cm kukula.

 

Nyerere (Iridomyrmex humilis) - zimagwira mazira omwe njuchi zaikira komanso ana a njuchi. Pewani nyerere popaka mafuta mawaya omwe tamangira mng’oma.

 

Nsabwe(Braula spp.) - zimadya zakudya zotsalira ku kamwa kwa njuchi. Pewani pofukiza utsi ku njuchi zomwe zili ndi nsabwe, nsabwezi zimagwa kenako mutha kubwezeretsa njuchi mu mng’oma..

Katumbu (Mellivora capensis) (chiuli) – ndi chilombo choononga chomwe chimaswa ming’oma ndikudya zisa zonse osalumidwa ndi njuchi. Mangani mpanda malo ozungulira ming’oma. Mangilirani ming’oma mmwamba osachepera mita imodzi. Onetsetsani kuti ming’oma isakhale pansi pa nthambi ya mtengo.

MATENDA NDI KAPEWEDE KAKE

European foul brood - Matendawa amafala ndi kachilombo kosaoneka ndi maso kotchedwa Bacteria. Amagwira ana anjuchi amasiku atatu. Pewani matendawa powotcha zisa zogwidwa ndi matenda komanso mungathe kupopera mankhwala.

 

Sac brood – matendawa amafala ndi kachilombo kosaoneka ndi maso kotchedwa virus. Amafanana ndi matenda a European foul brood.

American foul brood – ana anjuchi amafa masiku oyambilira ndipo amapanga madzi muzisa omwe amaoneka otuwa. Pewani matendawa powotcha zisa zogwidwa ndi matenda komanso mungathe kupopera mankhwala.