Module Articles

ULIMI WA NSOMBA

ULIMI WA NSOMBA

Kumanga mayiwe ansomba

Pamene mwasankha malo abwino oyikapo mayiwe anu, tsopano ndi nthawi yakuti mumange mayiwewo. Dziwani kuti pa nthawi imeneyi mukuyenera kukhala kuti mwasakha kale mulingo/kukula kwa mayiwe ansomba zanu

Kukonza pamalo omangapo mayiwe

  • Jambulani moyenera poyika zikhomo pa malowa molingana ndi makulidwe a mayiwe omwe mukufuna.
  • Chotsani mitengo, zitsamba komanso mizu yonse pamalowa
  • Dothi la pamwamba lomwe lili ndi chonde, ndi losayenera kumangira zikupa/khoma la mayiwe anu. Kombae, lisamaleni chifukwa lidzafunikabe kudzalithira pansi komanso mmbali mwa mayiwe mukamaliza kuwamanga ncholinga chakuti adzathandizire kukula kwa tizomera tammadzi tomwe nsomba zimadya.

Kukula kwa mayiwe ansomba komanso ma shape ake

  • Milingo ya mayiwe imasiyanasiyana motengera ndi kukula komanso kutsetsereka kwa malo ndi mulingo wa net yokololera nsomba. Koposaposa, ametengera momwe mlimi akufunira
  • Mayiwe a rectangle ndi abwino kwambiri. Kupatula kuti samavuta pokolola nsomba, mayiwe achonchi amathandiziranso kuti mpweya uzilowa mmadzi mosavuta makamaka pamene mulitali mwake mwalunjika kochokera mphepo

 

  

 

Kuzama kwa mayiwe

  • Mayiwe ansomba amakhala ozama mosiyanasiyana
  • Komabe zindikirani kuti mukamasankha kuzama kwa mayiwe ansomba zanu, kuwala kwa dzuwa kuzitha kukafika mpaka pansi penipeni pa mayiwe
  • Nthawi zambiri, kuzama kwa mulingo wa 1m komanso 1.5m ndikwabwino chifukwa kumapereka danga kuti kuwala kwa dzuwa kuzilowa mosavuta