Alipo matenda ochuluka komanso tizilombo tochuluka tomwe timagwira nsomba mmayiwe. Komabe ife tingokambiranako matenda ochepa chabe komanso tizilombo tochepa chabe tomwe/omwe amapezeka kwambiri kwathu kuno
Gas bubble disease
- Nthawi zambiri, makamaka pamene alimi aweta nsomba zochuluka kwambiri mmayiwe awo, amafuna kuti awonjezere mpweya womwe nsomba zimapuma pogwiritsa ntchito njira zina kupatula zachilengedwe. Pamene alimi akupanga izi, ndithu zimatheka kuthira mpweya wochuluka kwambiri mmayiwe zomweso zimayambitsa matendawa
- Matendawa zotsatira zake, amapha kwambiri nsomba zazing’ono ndi zazikulu zomwe mmalo oweteramo nsomba.
- Komabe alimi angapewe kuthira mpweya wowonjezera wochuluka kwambiri mmayiwe pogwiritsa ntchito njira zina zoyezera mpweya mmayiwe
Trichodina parasite
- Iti ndi tina mwa tizilombo tomwe timagwira nsomba mmayiwe.
- Tikagwira nsomba, timawononga khungu la nsomba komanso ma gills.
- Tizilomboti timagwira kwambiri Chambo, Chilungumi komanso Makumba omwe amawetedwa mmayiwe chifukwa cha kuthinana kuyerekeza ndi nsomba zomwezi koma zomwe zakulira mnyanja.
- Nsomba zazikulu ndi zomwe zimakhala pachiopsezo kuyerekeza ndi zazing’ono
- Pamenye nyengo ili yozizira kupangitsanso kuti mmadzi a mmayiwe akhale ozizira, ndipamene tizilomboti timatengerapo mwayi wofalikira kwambiri mmayiwe.
Zina mwa zizindikiro za tizilomboti mmayiwe ansomba
- Khungu la nsomba limakhala lowonongekha/tizilonda
- Ma gills a nsomba amakhala owonongeka/tizilonda
- Nsomba zimavutika mapumidwe
- Nsomba sizimakhala ndi chidwi chofuna kudya
Kapewedwe ka tizilomboti
- Alimi ayenera kupewa kuweta nsomba zochuluka/mothinana mmayiwe kuti apewe tizilomboti