Module Articles

ULIMI WA NSOMBA

ULIMI WA NSOMBA

Kasamlidwe ka mbeu

Pamene tafika gawo lino, ndiye kuti tamaliza kumanga mayiwe ansomba zathu ndipo madzi alowamoso kale. Chofunikanso kukumbukira nchakuti, tikamafika mgawo lino ndiye kuti mwapanga kale chisankho cha mtundu wa nsomba zomwe mukufuna kuweta. Komabe monga ndinafotokozanso kale, zokamba zathu muno zitenga chitsatso cha Chambo, Makumba ndi Chilungumi pokhalanso nsomba zomwe zimawetedwa kwambiri kuno ku Malawi.

  • Pezani tiyana tabwino ta nsomba zomwe mukufuna kuweta. Alipo malo ochuluka omwe mukhoza kupezako nzombazi. Ma farm ndi ma kampani oweta nsomba akuluakulu komanso mmasukulu opanga za ulimi wansomba ndi ena mwa malo omwe mungapezeko nsombazi.
  • Chambo, Chilunguni ndi Makumba ndi zina mwa nsomba zoyenera kuweta chifukwa zimachulukana kwambiri.
  • Ngati mwasankha kuweta nsomba zoti zimachulukana kwambiri, khalani osamala pofuna kusankha kuchuluka kwa nsomba zomwe muwete mmayiwe chifukwa zikachulukana kwambiri sizimakula bwino. Mwachitsanzo, kuweta nsomba zokwana zisanu (5) pa kamalo kokwana (1m x 1m) kungabweretse mavuto amenewa. Komabe, ngati cholinga cha mlimi nkufuna kudzakolola nsomba zosakula kwambiri, ndiye kuti kupanga izi kungakhale ndi phindu.
  • Kuweta nsomba ziwiri kapena zitatu pa malo a (1m x 1m), kumathandiza nsomba kuti zikule bwino ngakhale zakudya zitakhala zocheperapo
  • Onetsetsani kuti mwasankha njira yabwino yonyamulira nsomba zanu kuchoka komwe mwakatenga ncholinga chakuti zisafe.

Kudyetsera nsomba

Pamene mwaweta nsomba mmayiwe, kudyetsera nchinthu chofunika kwambiri kuti nsombazo zikule bwino.

  • Kwakukulu nsomba za Chambo, Makumba ndi Chilungumi zimadya kwambiri zomera ndi tizilombo zomwe zimakula mmayiwe. Nchifukwa chake kumbuyo kuja tinanena kuti pansi komanso mu zikupa za mayiwe ansomba zanu muthiremo dothi lomwe ndi la chonde ncholinga chakuti zomwera ndi tizilombo tikukambidwa panozi zithe kukula bwino.
  • Komabe ndi chithu chofunika nsomba ngati iz kuzipatsa zakudya zowonjezera monga madeya ndi zitosi za nkhuku mwa zina.
  • Zakudya zowonjezera zomwe mukuyenera kuzipatsa nsombazi, zikuyenera kukhala 3-5% ya kulemera kwa nsomba zonse zomwe mukufuna kudyetsera
  • Nthawi zonse, dyetserani nsombazi nthawi yofanana komanso pa malo amodzi

 

Kukolola nsomba

Pamene nsomba zakula mmayiwe, ndi nthawi tsopano yoti mukolore. Dziwani kuti nsomba zimafika nthawi yakuti sizimakulanso mmayiwe ngakhale mutapitiliza kuzipatsa zakudya choncho kuzikolola ndi chiganizo chabwino.

  • Nthawi zambiri, miyezi yokwana 5-6 kuchokera nthawi yomwe mudaweta nsomba mmayiwe, ndi yokwanira kuti mudziwe kuti nsomba zanu zafika pa mulingo wokolola makamaka ngati zawetedwa mu nyengo yotentha.
  • Miyezi yopitilira isanu ndi umodzi ndi yokwanira kuti mukolole nsomba zanu ngati zidawetedwa mu nyengo yozizira.
  • Kukolola nsomba zikafika pa mulingo wake kumachepetsa chiopsezo kwa akuba.
  • Alimi ayenera kugwiritsa ntchito ma net oyenera pokolola nsomba kapenanso kuphwetsako madzi mmayiwe ncholinga chofuna kuti ntchito yokolola isakhale yovuta kwambiri.

 

Tinyama tomwe timawononga nsomba

Panthawi yomwe alimi akuweta nsomba kuchokera pa nthawi yomwe adayika nsomba mmayiwe, pamapezeka tinyama tomwe timabwera kudzawononga nsambazi. Chocho alimi ayenera kukhala tchelu.

  • Mbalame monga dokowe (grey herons) mwazina, zimatha kubwera masana kudzawononga nsomba mmayiwe. Kusizilansa ndi miyala kapena kupeza njira ina iliyonse yomwe ingawopseze mbalamezi ingathandize.
  • Katumbu ndi kanyama kenanso komwe kamatha kuwononga nsomba kwambiri mmayiwe. Kusiyana ndi mbalame, kanyamaka nthawi zambiri kamadzawononga nsomba usiku. Ngakhale palibe njira yodalilika kwambiri yotetezera nsomba mmayiwe ku katumbu, kutchera misampha kungakhale kothandiza.
  • Munthu ngakhale kuti sitingamuyike mu gulu la tinyama towononga nsomba, koma nayenso amatha kubwera kudzawononga nsomba mmayiwe kudzera mu kuba makamaka pomwe nsomba zakula kufika pa mulingo wokolola. Komabe, kumanga mayiwe athu kufupi ndi nyumba zathu kungatipatse mwayi wochepetsa chiopsezo cha anthu akubawa.
  • Mbalame ndi akatumbu zili ndi kuthekera kowononga kwambiri nsomba mmayiwe choncho alimi sakuyenera kuzipatsa mpata.