Ulimi wa nsomba mwachidule ndiko kuweta nsomba mmalo osiyanasiyana monga mu mayiwe, hapa, cage ngakhalenso ma tank kungotchulapo malo ochepa. Ulimiwu, kwambiri umachitika ndi cholinga chofuna kupeza phindu. Pali mitundu yochuluka ya nsomba zomwe zimawetedwa pa ulimiwu, komabe pano tifotokonza za ulimiwu motengera ndi mitundu ya nsomba zomwe zimawetedwa kwambiri ku Malawi.
Mitundu ya nsomba
Pali mitundu inayi ya nsomba yomwe imawetedwa kwambiri muno mMalawi. Mitundu imeneyi ndi monga Chilungumi, Chambo, Makumba komanso Mlamba. Chambo, Chilungumi komanso Makumba ndi nsomba zomwe zimawetedwa kwambiri kuyerekeza ndi Mlamba.
Kuweta nsomba
Ngakhale kuti mitundu yambiri ya nsomba zomwe zimawetedwa kuno ku Malawi zikhoza kuwetedwa mmalo osiyanasiyana, kwambiri alimi ang’onoang’ono amakonda kuweta nsomba mu mayiwe. Mayiwe ansombawa amakhala osiyanasiyana. Pali mayiwe okulirapo komanso ocheperapo, onzama komanso ozama pang’ono. Ma shape awonso alipo osiyanasiyana komabe, mayiwe ozama mulingo wa 1m mpaka 1.5m ndi omwe amakondedwa chifukwa amapereka danga kuti kuwala kwa dzuwa kuzifika mpaka pansi penipeni pa mayiwe. Mayiwe a shape ya rectangle ndi abwino chifukwa amathandizira kuti mpweya uzilowa bwino.