Module Articles

Maphunzilo a Zachuma

Maphunzilo a Zachuma

Kusunga(Chichewa)

KUSUNGA

Kusunga ndikuyika ndalama kapena katundu monga chakudya, kaya ziweto mwapadera zodzagwiritsidwa ntchito mtsogolo.

Masungidwe a ndalama

  • e; iyi ndinjira yosungira ndalama mwachikale monga kusunga ndalama mokumbira pansi, kuika muchitini kapena kusungitsa kwa achibale

Kusunga modzera mu katundu; tithaso kusunga ndalama kudzera mu katundu monga ziweto pakhomo ngati ng’ombe, mbudzi kapena nkhuku.

  • ; iyi ndi njira yosungira ndalama motetezeka monga kusunga ndalama ku banki ndi mabungwe osunga ndalama ovomereka ndi boma.

Ndikofunika kuzindikira kuti ndalama imapezeka movutikira, kotero tisunge ndalama zathu kumalo omwe zikhale zotetezeka komanso komwe zingathe kulandila chiongoladzanja monga ku banki

Nchifukwa chiyani anthu amasunga ndalama

  • Kukonzekera zinthu zogwa mwadzidzidzi monga maliro, matenda ndi zina
  • Kukonzekera zochitika mtsogolo monga kulipilirana sukulu, maukwati kapena ulimi
  • Kukonzekera maziko amtsogolo monga kumanga nyumba, kugula malo, njinga kapenanso feteleza

Zolepheretsa kusunga

  • Kupeza ndalama mochepekedwa
  • Kuchuluka kwa zofunika kugwiritsa ntchito ndalama
  • Kuchuluka kwa mavuto okugwa mwadzidzidzi

Zofunika kudziwa posunga

Choyamba, tidziwe cholinga chosungira ndalama komanso kuti tikuyenera kusunga ndalama zingati ndipo kuti zifunika liti. Izi zitithandiza kudziwa kuti titha kumasunga ndalama zingati pa sabata kapena pa mwezi.

Pomaliza dziwani kuti munthu aliyense atha kusunga ndalama ngakhale amene amapeza ndalama zochepa malinga mtima wake wafunitsitsa kusungako.