Module Articles

Maphunzilo a Zachuma

Maphunzilo a Zachuma

Kuyika masopwenya achuma

MASOMPHENYA
Masomphenya/ ndi malingaliro/ maloto/ kapena zolinga zomwe munthu amalakalaka atadzakwanilitsa pamoyo wake/ kapena pabanja lake//

Zina mwazitsanzo za masomphenya ndi monga; kumanga nyumba ya makono, kuphunzitsa ana sukulu, kugula feteleza komanso kuyamba kapena kukuza bizinesi

Mitundu ya masomphenya

Pali masomphenya omwe tingathe kuwakwaniritsa pompopompo monga/ kugula chakudya pakhomo/ ena amakwaniritsidwa mwakanthawi koma osadutsa zaka 5 monga kulipila sukulu ya mwana// Mtundu wina wa masomphenya ndi wa masomphenya omwe amakwanilitsidwa patantha nthawi yayitali kupitilila zaka 5 monga kumanga nyumba yamakono ya zones momo

Tingakwanilitse bwanji masomphenya athu

Choyamba tidziwe zinthu zones zofunika kuti tikwanilitse masomphenyawo monga ndalama/ zipangizo/ ndi zina Zotero//

Chachiwiri tidziwe zipangidzo zomwe tilinazo ndi zomwe zifunike kuti tiwonjedzere pokwanilitsa masomphenya.

Kenako tipange dongosolo la mmene tipezele zinthu zowonjedzerazo ndi cholinga choti tidzakwanilitse masomphenyawo.

Komanso ndikofunika kwambiri kuzindikira kuti pali zinthu zina zomwe zingathe kulepheretsa kapena kusokoneza masomphenya monga matenda, imfa, kusachita bwino kwa mbeu kumunda, komanso kusayika chidwi pa masomphenya athu//

Kupanga zisankho zoyenera ndi ndalama zathu

Tizindikire kuti pamoyo wamunthu pali zinthu zina zofunika kwambiri monga zakudya pakhomo/ zovala/ komanso nyumba// Ndipo pali zina zofunika mongokometsa moyo monga/ kanema/ galimoto/ njinga, kapena wailesi. Pamene tikupanga masomphenya ndibwino kuyambira zinthu zofunika kwambiri pamoyo ndikumalizira ndi zomwe zili zongokometsa moyo