Module Articles

Maphunzilo a Zachuma

Maphunzilo a Zachuma

Bajeti

BAJETI

Bajeti ndi dongosolo la zachuma lomwe limafotokozera kochokera kwa ndalama komanso mmene ndalamayo ingagwilitsidwire ntchito panyengo kapena nthawi yomwe takhazikitsa

Kufunika kwa bajeti

  • Kudziwa mmene tingagwilitsire ntchito ndalama zathu ndikupanga zisankho zoyenela
  • Kugwiritsa ntchito ndalama mosamala ndi mwadongosolo
  • Kuti tizilamulire ndi kuzitetezera ndalama zathu
  • Kuti tikwanilitse masomphenya amtsogolo

Kapangidwe/kalembedwe ka bajeti

Popanga bajeti ndibwino kulingalira mofatsa njira zonse zomwe timapezera ndalama monga kuchokera ku bizinesi, kugulitsa ziweto, ganyu, komanso zopatsidwa ndi abale.

Chachiwiri, tilingalire njira zonse zomwe tingagwiritsire ntchito ndalamzo. Ndalama zimatha kutuluka pogula zosowa pakhomo, zipangizo zakumunda, kulipira ana sukulu ndi zina zotero.

Komanso, pamene tipanga bajeti ndikofunikira kulingalira ndalama zomwe tingasunge pofuna kukwaniritsa zokhumba zina zamtsogolo. Kuti tikwanilitse masomphenya akusunga, tikuyenera kuzindikira kuti ndalama zotuluka zisapitilire ndalama zomwe timapeza

Pomaliza, bajeti ndiyofunika kwambiri pa moyo wathu ndipo imatithandiza pamene tikufuna kukwaniritsa masomphenya athu. Choncho onetsetsani kuti mukudziwa bwino dongosolo la kayendetsedwe ka chuma chanu