Anthu amabwereka zinthu zosiyanasiyana monga/ zakudya/ zipangizo zakumunda/komanso ndalama//
Tingathe kubwereka ndalama kumalo monga; Ku banki, kumagulu osunga ndikubwerektetsa ndalama komanso kwa achibale, anzathu ndi kwina kwambiri
Nchifukwa chiyani anthu amabwereka ndalama
- Kuthetsa mavuto ogwa mwadzidzi monga maliro, matenda, ndi zina zotero.
- Kulowetsa ku bizinezi kapenanso kupangira mazko monga kugula malo kapenanso munda
- Kugula katundu wosiyanasiyana wa pa banja woti mtengo wake ndiwoposera ndalama zomwe timapedza monga kugula ngolo, kapena njinga
Dziwani kuti sichanzeru kwenikweni kubwereka ndalama ndicholinga chogula zakudya/ kupangila ziliza kapenanso ukwati// chifukwa ndizovuta kubweza kwake. Ndikoyenera kulowetsa ndalamazo ku bizinezi chifukwa bizinezi ikhoza kubweza ngongole//
Udindo wa wobwereka ndalama
- Kubweza ngongole pa nthawi yake chifukwa zimakhala ndi mavuto ake monga kulipira chindapusa
- Kutenga ngongole yomwe mungathe kubweza mosavuta
- Kubweza pa nthawi yake ndi chiwongoladzanja chomwe
Zotsatira za kulephera kubweza ngongole
- Munthu amataya mwayi wa ngongole ina mtsogolo
- Mbiri yako imayipa
- Komanso kulandidwa katundu
Mungatenge ngongole yochuluka motani
- Kutenga ngongole yodutsa ndalama zomwe mumapeza zimabweretsa chipsinjo pa moyo wanu
- Ngongole yanu isadutse 30% ya ndalama zomwe mumapeza
Zofunika kudziwa musanatenge ngongole
- Tsiku loyenela kubweza ndalama komanso chiwongola dzanja choyenela kupelekedwa
- Onetsetsani kuti chomwe mukufuna kugula chidzakubweretserani ndalama kwa kanthawi ndithu
- Katundu wogulidwa adzapanga ndalama yochuluka yokwanira kubweza ngongoleyo
Pomaliza, dziwani kuti ngongole ndi chikakamizo kuti mukatenga mukuyenera kukabweza ndithu