Chinangwa ndi mbewu imodzi ya mgulu la mbatata. Ndichofunikira chifukwa timapezamo chakudya, ndalama komanso mbewu. Chinangwa chimabzalidwa moonjezera mmadera amene chimanga sichimachita bwino. Madera a m’mphepete mwanyanja monga Nkhotakoata, Rumphi komanso madera awa, Kasungu, Mzimba, Lilongwe, Dedza, Dowa, Machinga ndi Mulanje chimabzalidwa ngati mbewu yochepetsa chilala. Masamba achinangwa ndi ndiwo komanso chakudya cha ziweto.
Pomaliza pa phunzilori alimi akuyenera kudziwa:
Mitundu yachinangwa ilipo khumi ndi iwiri, ina mwa iyo ndi iyi;
DZINA |
MAKOMEDWE |
Nthawi yonkwimira (miyedzi) |
KHOLOLA (mt/Ha) |
Manyokola/Mbundumali |
yozuna |
9-15 |
25 |
Gomani |
yowawansa |
9-15 |
25 |
Chitembwere |
yowawansa |
15-18 |
18 |
Silira |
yowawansa |
12-15 |
25 |
Maunjili |
yowawansa |
9-12 |
35 |
Mkondezi |
yowawansa |
9-15 |
40 |
Sauti |
yowawansa |
12-15 |
25 |
Yinauti |
yowawansa |
12-15 |
25 |
Phoso |
Yowawansa |
12-15 |
35 |
Mulola |
Yowawansa |
12-15 |
40 |
Sagonja |
Yowawansa |
9-12 |
35 |
Chiombola |
Yowawansa |
9-12 |
45 |
Mbundumali |
|
|
|