Module Articles

Chinangwa

Chinangwa

Kukolola

  • Dulani mtengo wachinangwa kuchokera 30cm mpaka 50cm   kuyambila pansi pa mtengo kuti mokolore bwino.
  • Chinangwa chimakololedwa nthawi ili yonse malinga ndi mtundu wake.
  • Kukolola chinangwa ndikosavuta nyengo ikakhala ya mvula komanso dothi la mchenga pogwilitsira ntchito manja.
  • Chinangwa chimaonongeka chikakololedwa, choncho alimi kololani mulingo wofunikira.
  • Kumbani mozungulira mtengo wa chinangwa kuti muzule bwino.
  • Konzani chinangwa nthawi yomwe mwakolola.

Kukoza chinangwa

  • Makaka, ufa kapena masamba a chinangwa amapangila zinthu izi;
    • Kuchepesa poizoni
    • Kufewetsa
    • Kukoza kholora owonongeka kupanga chakudya chomwe chimasungidwa nthawi yayitali.
  • Ku mbewu zozuna, pangani makaka ngati ali okudya
  • Kwa mbewu yowawa, vikani makaka m’madzi. Njila imeneyi imasatidwa m’maboma monga  Mulanje, Nkhotakota ndi Nkhatabay   
  • Alimi ali olimbikitsidwa kusunga kholora wa  chinangwa  mu m’mtundu wa ufa komanso makaka

kusenda

  • Kuti mupange makaka kapena ufa, chinangwa chimasendedwa kaye.
  • Sendani pogwilitsira ntchito mpeni. Ntchito yimatenga nthawi ndithu koma imapatsa zotsatila zabwino

Kuteteza zokolola

  • Thilani akiteliki popewa anankafumbwe.
  • Mulingo wa 25g wa akiteliki mukhoza kuthira ku kholora wa 50kg.