Chinangwa
Matenda Ndi Tizilombo
Khate
- Matendawa amafala ndi kachilombo kosaoneka ndi maso kotchedwa virus komanso gulugufe oyera.
- Masamba amakhala amawanga komanso opiringizana.
Kuchepetsa
- Bzalani mbewu ya ukhondo
- Zulani ndikutentha mitengo yogwidwa ndi matenda
Chiwawu
- Nthendayi imaumitsa masamba ndipo mbewu imafa.
Kuchepetsa
- Otchani komanso kwilirani mitengo yogwidwa ndi nthendayi.
- Bzalani mitengo ya mphamvu.