Chinangwa
Kasamlidwe ka mbeu
KUKONZA MUNDA
- Galauzani munda 15cm kapena 30cm kawiri musanabzale chinangwa.
- Pangani nthumbira ndi mizere m’dothi la chinyontho.
- Kumadera a chigwa, alimi amakonza mizere, kapena nthumbira pofuna kupewa madzi.
- M’madambo, mbewu yachinagwa imabzalidwa m’mizere ya m’mwamba komanso yayikuluikulu yotalikilana 120 cm kuti dothi lisamwe madzi.
- Konzani mizere yotalikilana ndi 90 cm komanso yokwera 30cm
KUKONZA MBEWU
- Dulani mbewu pamene mwakonzekera kubzala.
- Dulani mitengo ya mbewu ndi mpeni osongoka kapena chikwanje.
- Dulani mitengo yambewu yotalika 25cm kapena 30cm.
- Dulani mitengo ya mbewu yonenepa osati yoonda.
- Dulani mbewu kuchokera pansi mpakana pakati ku mtengo wosapitilira miyezi isanu ndi inayi(9) mitengo ya mbewu ikhale ya thanzi
- Bzalani mipukutu yosachepera 65 osapitirira 80, mitengo yake yotalika ndi 50cm.
- Bzalani ndi mvula yoyambilira.
- Bzalani mbewu mnthaka.
kupalira
- Palirani mwachangu udzu ukangomera makamaka mu miyezi itatu yoyambilira.
Tizilombo
Nsabwe zoyera
- Tizilomboti timavuta kwambiri m’dziko lino pochepetsa mapando a mitengo ndi kupinimbira kwa mbewu komanso mbewu zimafa.
- Yenderani mbewu yanu kawirikawiri, kuti muone ngati yagwidwa ndi tizilomboti
Nsabwe zoyera
- Pobzala mitengo mofulumira, yamphamvu ndi yaukhondo
- Pewani kulowetsa mitengo yogwidwa ndi tizilomboti m’munda.
Gulugufe Oyera
- Tizilomboti timafalitsa matenda a khate.
- Kuchepetsa kwake ndikuchiza matenda amene tizilomboti timayambitsa komanso pobzala mitengo ya ukhondo.
Nkhono zamchinangwa
- Tizilomboti timagwira nthambi komanso masamba
- Tizilomboti timayamwa mtengo.
- Tizilomboti timasintha masamba kuchoka kobiliwira kupita kuchikasu.
Kangaude wobiliwila
- Kachilomboka kamafala kwambiri mnyengo ya dzinja ndipo kamadya mitsitsi yaying’ono ndi yofewa. Timachepetsa chiwerengero cha masamba komanso kupangitsa masamba kukhala a chikasu.
- Bzalani mofulumira mbewu yopilira komanso ya mphamvu.