1.0 MAU OTSOGOLERA
Pafupifupi alimi oposa 80% ku Malawi amalima nyemba, pambali pa mbewu zina monga chimanga, chinangwa, soya mtedza ndi zina. Nyemba zimadyedwa ngati Khwanya, Zitheba, zaziwisi kapena zouma.
Cholinga chachikulu ndikuthandiza alimi kuti akhale ndi ukadaulo ndi nzeru pakalimidwe ka Nyemba.
Pomaliza pa phunziroli alimi akuyenera kudziwa izi:
- Kukhala ndi nzeru zopititsira patsogolo ulimi wa nyemba.
- Kasamalidwe kabwino ka nyemba.
- Njira zochepetsera kapena zogonjetsera tizilombo ndi matenda.
- Mmene angasamalire nyemba nthawi yokolola, ya kudya komanso yogulitsa.
2.0 NYENGO YOYENERA PA ULIMI WA NYEMBA
- Kutentha - Nyemba zimafuna nyengo yotentha kwa mulingo wokwana150C mpaka 250C.
- Dothi - Nyemba zimafuna dothi labwino losakanikirana ndi mchenga komanso losachita lowe.
- Mvula - Nyemba zimakula bwino ndi mvula yochuluka yokwana 300mm mpaka 500mm pa chaka.
3.0 MITUNDU YA NYEMBA
- Nyemba zazifupi (Mkhalatsonga),
- Nyemba zoyanga komanso zazitali
- Nyemba zapatikati
3.0.1 Nyemba zazifupi
- Nasaka –zooneka ngati ipso
- Bwenzilawana- za khungu la chikasu komanso zobulungira
- Kamtsilo – khungu lake lofiira komanso zooneka ngati ipso
- Saperekedwa / sapatsika – khungu lake lofiira komanso zooneka ngati ipso
- Napilira- za khungu lofiira koma zamawanga oyera
3.0.2 Nyemba zoyanga komanso zazitali
- Kanzama – khungu lake lofiira komanso zobulungira
- Namajengo – khungu lake lofiira komanso zooneka ngati ipso
3.0.3 Nyemba zapakatikati
- – khungu lake la mawanga ofiira ndi oyera
Nagaga - khungu lake la khaki komanso zooneka ngati ipso
- - khungu lake la khakhi ndizooneka ngati ipso
- - khungu loyera ndi mawanga ofiira
Mitundu ina ndi iyi: Kabalabala, Kamtauzgeni, Nyauzembe, Phalombe, Salanje, Khalira, Kalima, Kabulangete, Kambidzi ndi Kayera