Module Articles

Nyemba

Nyemba

Matenda Ndi Tizilombo

Kodikodi imafala ndi Nsabwe, masamba amakwinyika ndipo nyemba zimakanika kukula. Bzalani mbewu zopilira kumatendawa. Chiwawu chimafala ndi kachilombo kosaoneka ndi maso kotchedwa bacteria. Izi zimachepetsa zokolola. Bzalani mbewu mwakasinthatsintha, mwansanga, komanso mbewu zopilira kumatenda, kwilirani zotsalira za mbewu, poperani mankhwala a Daconil.

Tizilombo toononga nyemba ndi monga;

Nankafumbwe – amaboola nyemba zouma ndipo zimatulutsa ufa, tetezani nyemba pothira mankhwala a Actellic.

Chikumbu – zimaboola nyemba zamakoko komanso masamba ndipo zimachepetsa zokolola. Poperani mankhwala a Carbaryl.

Nsabwe – zimaumitsa mbewu chifukwa zimayamwa madzi a munyemba ndipo zimachepetsa zokolola. Poperani mankhwala a Dimethoate.

Mbozi – zimaumitsa tsinde, mbewu zimakanika kukula ndipo zokolola zimachepa. Bzalani mbewu mwansanga.