Sankhani nyemba pokolola ngati zidabzalidwa mosiyanasiyana kapena ngati ndi zamitundu yosiyanasiyana. Musakolole kuli dzuwa kuopetsa kuthetheka kwa nyemba. Gwiritsani ntchito chisikiro podula tsinde la nyemba kapena zulani ndi manja. Kololani nyemba pamene zakhwima bwino. Yanikani nyemba pa pepala kapena pamphasa. Ombani ndi manja pamene zauma pogwiritsa ntchito kamtengo. Petani nyemba kuti muchotse makoko. Chotsani miyala, dothi, zophwanyika, zamatenda ndi zina zonse komanso sankhani molingana ndi mtundu wake.
Sungani nyemba mzipangizo zosungiramo monga matumba, mbiya ndi zipangizo zina. Musaphatikize mbewu yokolola chaka chino ndi mbewu yokololedwa chaka chatha posunga. Thilani Actellic kuti zisaonongeke ndi namkafumbwe kapena ngati mbewu yisungidwe kwa nthawi yayitali. Sungani matumba a nyemba pamalo okwererako otalika mita imodzi ndipo asakhudzane ndi chipupa. Sungani matumba anyemba pa malo osadotha.