Nyemba zolimidwa mophatikiza ndi mbewu zina zimayenera kubzalidwa pamene mbewu inayo yamera kumene. Nyemba zobzalidwa pazokha zimayenela kubzalidwa pakatikati pa Disembala mpaka pakatikati pa Januwale m’chigawo chaku mmwera komanso mwezi wa Januwale m’chigawo cha pakati ndi ku mpoto. Nyemba zobzalidwa mochedwa pamene mbewu inayo yakula zimayenera kubzalidwa mwezi wa Febuluwale kapena mwezi wa Malichi. Nyemba zobzalidwa nthawi ya mthilira zimayenera kubzalidwa pamene mbewu zina zonse zakololedwa m’munda. M’mbali mwanyanja, mbewuyi imayenera kubzalidwa miyezi ya Meyi ndi Juni, pamene kumalo okwera imayenera kubzalidwa miyezi ya Julaye mpaka Ogasiti pamene kwayamba kutentha.
Kuchuluka kwa mbewu
Kuti alimi akolole zochuluka ndi zokwanira ayenera kubzala nyemba pa mulingo woyenera pa ekala kapena pa hekitala. Nyemba zazifupi zimafunika 70kg kapena 80kg pa hekitala. Nyemba zoyanga zimafunika 75kg kapena 90kg pa hekitala. Nyemba zolimidwa mophatikiza ndi mbewu zina zimafunika 50kg kapena 60kg pa hekitala. Nyemba zakudimba zimafunika 40kg kapena 50kg pa hekitala.
Kupalira
Munda wa nyemba umayenera kukhala wopanda udzu makamaka masabata asanu ndi imodzi oyambirira pamene mbewu yabzalidwa. Kupalira pafupipafupi mkofunikira chifukwa kumachepetsa mpikisano wa zakudya pakati pa mbewu ndi udzu. Palirani mbewu pozula udzu ndi manja kapena makasu. Kugwiritsa ntchito mankhwala opha udzu ndi njira ina yopalirira mmunda wa nyemba. Sibwino kupalira nyemba zitayamba kale maluwa chifukwa maluwa amayoyoka ndipo zimachepetsa zokolola. Zikirani mitengo nyemba zoyanga kuti zisagwe ndiponso kuonongeka.
Kuthira Feteleza
Thirani Feteleza woyamba wa 23:21:0+4S (wokulitsa) pa mulingo wa 100kg pa hekitala pamene mukubzala. Feteleza wachiwiri (wobereketsa) wa UREA amathiridwa mukamaliza kupalira koyamba. Ngati feteleza palibe alimi akuyenera kuthira manyowa