Nzama ndi imodzi mwa mbewu zofunika kwambiri mdziko muno imene imakondedwa ndi anthu ambiri, ikhoza kuphikidwa ngati ndiwo kudyedwa payokha komanso imathandiza kubwezeretsa michere yofunika m’nthaka. Nzama zimachita bwimbo ngakhale mvula igwe yochepa.
Cholinga chachikulu ndi kupititsa patsogolo ulimi wa mbewu ya nzama madera onse omwe imalimidwa
Pomaliza pa bukuli mlimi ayenela kudziwa izi:
Kasamalidwe kabwino ka nzama, njira zochepetsera tizilombo ndi matenda a nzama, kudziwa m’mene angasamalire nzama pa nthawi yokolola mpaka nthawi yogulitsa.
Kayera – amakula bwino mmadera ambiri mdziko muno ngakhale panthaka yoguga, salira mvula yambiri
Makata - amakula bwino mmadera ambiri mdziko muno ngakhale panthaka yoguga, salira mvula yambiri
Kadziunde – yopilira kuchilala komanso imakula bwino mmadera onse mdziko muno.