Module Articles

Nzama

Nzama

Kasamlidwe ka mbeu

Kololani nzama zimacha (pamene mkati mwake mukuoneka timizera ta bulauni ndi masangwi akayamba  kuwoneka  chikasu). Zulani nzama pogwiritsa ntchito manja tolerani nzama zokhalira munthaka pokumba ndi khasu. Thotholani nzama pogwiritsa ntchito manja ndipo yanikani pamalo aukhondo kuti ziume. Yanikani mpaka nzama zidzimveka kugwedera mkati. Nzama zisungidwe muchipinda cha mpweya wabwino ndiponso chomangidwa bwino. Sungani zosaswa kuti zisagwidwe ndi namkafumbwe.