NDONDOMEKO YOSUNGA NDI KUBWEREKANA NDALAMA PAGULU
Pali magawo atatu a ndondomeko ya kusunga ndikubweleketsa ndalama:-
A. Kukonzekera kukhazikitsa ma S4T
Alangizi amayambila kupangitsa misonkhano m’midzi kudziwitsa anthu za ntchito yosunga ndi kubwerekana ndalama (S4T) kwa nthawi ya pakati pa mulungu umodzi (1) ndi itatu (3). Misonkhanoyi imachitika mmagawo awiri:
- Kukumana ndi mafumu komanso alangizi aboma ndi mabungwe ena kuwadziwitsa za pulogalamuyi.
- Kukumana ndi anthu onse mmudzi umene umakozedwa mogwirizana ndi a mfumu a mudzi pomwe alangizi amalongosola mwachidule dongosolo lonse la S4T. Anthu amene akhutila ndikufuna kupanga gulu nthawi yomweyo amatha kupanga magulu awo ndikulembetsa kwa mlangizi.