Module Articles

Ulimi Waziphukira Za Mitengo Yachilengedwe

Ulimi Waziphukira Za Mitengo Yachilengedwe

Zoyenera Kutsatidwa Pakasamalidwe Kaziphukira(FMNR)

  1. Kupanga kafukufuku waziphukira/ kapena zitsamba zachilengedwe zomwe zikugwirizana ndimapulani alimi komanso ziphukira  zamphamvu/ zoyenelera kapena zopeleka chiyembekezo// Izi zimachitika pozindikira kuti ziphukira zina zimaoneka ngati zitsamba zamaluwa chabe/ kapena zosafunikira ndiye mlimi ayenela kudziwa mitundu ya mitengo yachilengedwe yomwe akuyifuna kapena yomwe imakula mosavuta kapena mofulumira m’dera lake// Chisankho ichi chichokere pazolinga ndinso ubwino omwe mlimi waupeza kapena kuwudziwa pankhani yosamalira nkhalango zachilengedwe//
  2. Mlimi awerenge ziphukira 40 zomwe zikuyenera kusankhidwa pa hekitala imodzi kapena 40 pamayekala awiri ndi theka(2.5acres) kuti zikule pa malo omwe akufuna kuti akhale Nkhalango yake. Iyi ndi nthawi yomwe mlimi ayenera kutsimikiza mtundu wa mitengo yomwe wasankha kuti idzakhale gawo la nkhalango yake. Mitengo yayitali komanso yowongoka ndimene imasankhidwa.
  3. Mlimi adule ziphukila zonse zosasankhidwa ndi mpeni kapena chikwanje chokuthwa mochipititsa m’mwamba komanso chitayang’ana kumwamba kuteteza kuti nthambi isakhadzukire. Zipangizo zonse zogwilitsira ntchito/zikhale zokuthwa.
  4. Ziphukira kapena zitsamba zonse zomwe zasankhidwa komanso kuwerengedwa zisadzilidwe kapena kuphatiliya (kapena kuti Kuchotsa nthambi zina zosayenela kapena zosafunika zosapitilira zisanu (5).  Panthawi yomwe mitengo ili yaying’ono, kusadzila kuchitike pa mlingo wa theka(1/2) kuchokera kansi pa mtengo uliwonse.
  5. Kuteteza mitengo yomwe yasankhidwa komanso kusadzilidwa/kuphatiliya ndiudindo wa mlimi komanso anthu onse omuzungulira. Chifukwa chake kusamalira ziphukira ndi udindo wa munthu aliyense osati m’modzi. Izi zingatheke pogwira ntchito ndi Boma komanso mafumu ndi azitsogoleri a m’mudzi pokhonza malamulo oyendetsera nkhalango za m’mudzi.
  6. Ndiudindo wa mlimi, anthu a m’mudzi kapena dera Kulambulira m’mbali mwa nkhalango(fire-break) kuti mitengo yachilengedweyi itetezedwe.
  7. Malamulo a Nkhalango yachilengedwe ayenera kutsimikizira ndondomeko zotetezera moto kapena ziweto ndipo pakhale chindapusa chokhwima kwa onse olakwira lamulo