Ulimi Waziphukira Za Mitengo Yachilengedwe
Kusankha Malo Omwe Tingasandutse Nkhalango Yachilengedwe (FMNR)
- Malo ena aliwonse atha kukhala oyenera ngati pali ziphukira kapena zitsamba zachilengedwe zomwe ndizofunika komanso zikuphukira.
- Nkhalango yachilengedweyi itha kukhala m’munda wa mlimi, malo odyetsera ziweto, nkhalango yakale yomwe inawonongedwa, malo a miyala omwe salimidwa, pafupi kapena kuseli kwa nyumba ndinso malo ena omwe mudzi ungasankhe.
- Malingaliro kapena kaganizidwe kakasintha, munthu aliyense akhoza kusankha malo ndikutengapo mbali posamalira ziphukira.
- Njira iyi ndiyosaboola mthumba chifukwa imagwirizana ndikuthekera kwa alimi ambir