Module Articles

Ulimi Waziphukira Za Mitengo Yachilengedwe

Ulimi Waziphukira Za Mitengo Yachilengedwe

Mau Otsogolera

FMNR ndi kasamalidwe ka ziphukira za mitengo ya chilengedwe// Alimi ali ndiudindo wosankha malo omwe angathe kukhala nkhalango ya banja/ mudzi/ kapena dera// Iyi ndi njira imodzi yosamalira chilengedwe kuti mitengo ikule komanso itetezedwe// Njirayi imathandiza mitengo kukula mofulumila kusiyana ndikufesa mbewu za mitengo zomwe nthawi zambiri zimafuna ndalama zambiri/ komanso yambiri imafa. Njira iyi yosamalira Ziphukira/ imagwiritsa ntchito mwayi wa nkhalango yobisika m’nthaka//

Mlimi akasankha malo oyenelera/ amayenela kusankha ziphukira kapena zitsamba molingana ndi zolinga za nkhalango yake/ komanso amasankha ziphukira zomwe zikuoneka za mphamvu/ zowoonga bwino kapena zosangalala zomwe zikuyenera kusadziludwa bwino pochotsa mphanda zina zosayenera/ komanso mitengo yosayenera yomwe yayandikira kwambiri//