Chitani moyelekeza/ mtengo wogulitsira mbeu zanu: Gawani ndalama zonse zomwe mwalowetsa pa ulimi wa mbeuyo ndi malingana ndi kuchuluka kwa zokolola za mbeuyo; wonjezanipo phindu loyambira pa 15% kuti mupeze mtengo wogulitsira mbeu yanu.
Chepetsani kuola kwa mbeu: pindani mapesi kuti chimanga chizolike pansi ndipo madzi a mvula akhe bwino; Kololani mbeu za m’gulu la nyemba ndi kuziumitsa bwino ndipo tetezani mbeu ku mvula kapena chinyontho.
Kololani mbeu zikakhwima ndikuziumitsa pa mphasa, mkeka, kapena lona mpaka mbeu ziumitsitse (14%) kuti muchepetse nkhungu ndi chuku kuononga mbeu.
Pezani mankhwala kuchokera kwa wogulitsa/wopereka wodalirika kudzera m’gulu la alimi ndipo agwiritseni ntchito potsatira ndondomeko zolembedwa pa chikutiro.