Module Articles

CHUKU

CHUKU

Kuthana ndi chuku mu mtedza - Momwe mungachepetse kuipitsidwa kwa chuku

Kuchuluka ndi kufala  kwa fangasi ndi kuipitsidwa ndi aflatoxin mu mbewu kumachitika chifukwa cha zinthu zingapo: zina zimakhala zachilengedwe pomwe zina ndi zogwirizana ndi kasamalidwe ka mbewu. Alimi sangathe kuchitapo kanthu pa zachilengedwe; komabe, atha kusintha njira zaulimi zomwe zimagwiritsidwa ntchito polima mbewu kuti muchepetse matenda a fangasi, kukula ndi kupanga kwa aflatoxin.

Njira zosamalira mbewu zomwe zimachepetsa matenda m'munda

Njira izi zikulimbikitsa kuchepetsa kwa kugwidwa ndi fangasi mbeu zili mmunda.

 • Kubzala koyambirira: Kubzala koyambirira kumathandizira mbewu kuti ithawe chilala cha kumapeto kwa nyengo ya mvula chomwe chimapangitsa kuti makoko aume komanso achite ming’alu zomwe zimaika mbeu pa chiopsezo chogwidwa ndi fangasi otchedwa A.flavus.

• Kuonetsetsa ukhondo wa m'munda: Kupalira munthawi yake kumathandiza kuti nthaka ikhale chinyontho chofunikira kuti mbewu zikule bwino komanso kupewa kupewa kutha kwachinyontho mmunda zomwe zimapangitsa kuti makoko a mbeu achite ming’alu. Kuteteza mbeu ku chiswe ndikofunikira kuti mbeu zisalumidwe ndikuikidwa pa chiopsezo chogwidwa ndi fangasi.

• Kukolora madzi m'munda: Chilala chimaonjezera chiopsezo cha matenda a fangsi mmunda. Alimi ayenera kuonetsetsa kuti amasunga chinyontho m'minda yawo. Kugwiritsa ntchito mizere yomangiriridwa (mizere yamabokosi) kumathandizira kudikha kwamadzi mu dothi, potero kumachepetsa kufalikira kwa matenda a A.flavus. Mizere ya mabokosi iyenera kuikidwa koyambirira kwa nthawi yobzala kuti madzi azungike ndikuchepsetsa mavuto obwera chifukwa cha ng’amba. Kuphimbira mbeu kumathandizanso kuti madzi asungidwe.

• Kusintha nthaka: Kugwiritsa ntchito laimu ku mbewu kumathandizira kuti makoko akhale olimba. Makoko olimba amapereka chitetezo choyambalira ku matenda a fangasi.

Njira zosamalira mbeu zomwe zimachepetsa matenda pokolola

Izi ndi njira zomwe zimachepetsa chiopsezo chogwidwa ndi  matenda pochepetsa chiopsezo choti mbeu kapena makoko asweke ndikupereka mpata ku tizilombo ta fangasi.

• Kukolora mbeu zikafika pa nsikhu oyenera: Maso osakhwima amakhala ndi chinyezi chambiri ndipo amathandizira kufalikira ndikukula, ndi kuipitsidwa ndi aflatoxin. Chifukwa chake, kukolola pa nthawi yoyenera pomwe mbewuyo yakhwima kumachepetsa chiopsezo choti  mbewuyo ingakumane ndi kutentha kwambiri, mvula yadzidzidzi kapena chilala, zomwe zimathandizanso kumatenda.

Kupewa kuononga makoko: Muyenera kusamala mukamagwiritsa ntchito makasu kuti musaononge makoko. Kukolola moyenera, mlimi ayenera kukumba molambalala mizu kuti asaononge mtedza uli mmakoko.

Kuchotsa dothi: Ndikofunika kuchotsa dothi lonse lomwe limatsalira kuizu m'nthawi yokolola kuti mupewe kunyamula fangasi kupita naye Kumalo osungira mbeu ndi malo opangira zinthu kuchokera kumbeu.

Njira zosamalira mbewu zomwe zimachepetsa kuipitsidwa mukakolola.

Kasamalidwe ka mbeu vuto linanso lalikulu pa matenda a fangasi. Njira zomwe alimi ayenera kutsata zitha kuikidwa mmagawo awiri:

Pakhomo.

• Kuyanika koyenera: Kuyanika padenga kapena pamtunda kumayambitsa chinyezi ndipo kumathandizira kukula kwa fungus komwe kumayambitsa kuipitsidwa kwa aflatoxin. Kugwiritsa ntchito kwa Mandela Corks (podutsa mpweya wabwino) ndi njira imodzi yabwino kwambiri youmitsira mtedzai ndipo imakondedwa kwambiri chifukwa imachepetsa kuombedwa ndi dzuwa.. Mandela Corks  akuyenera kumangiriridwa pa pulatifomu yokwezeka, kusiya malo opanda kanthu pakati kuti mpweya uziyenda bwino mkati mwa chipangizocho.

• Kusenda makoko koyenera: Kuwaza madzi pa makoko posenda kumaonjezera chinyezi, izi zimaika pachiopsezo chogwidwa ndi mafangasi. Ndikofunika nthawi zones kuti musanyowetse makoko posenda. Kugwiritsa ntchito masheluche amakina kumathandizanso kuchepetsa ndalama zogwirira ntchito.

• Kusankha mbeu ndikusiyanitsa magiledi: Fangasi amalowerera mosavuta mu makoko osweka kapena owonongeka. Alimi ayenera kutchotsa mbeu za maso ang’onoang’ono, zosweka komanso zokwinyika.

Kusungidwa poyenera:Pamene tizilombo talowa mumbeu, timapangitsanso kuti fangasi apeze polowera, ndipo pamapeto pake aflatoxin amaipitsa zokolora zathu. Zokolora ziyenera kusungidwa pamalo owuma komanso otetezeka pomwe kulowa kwa tizilombo ndi chinyezi sikungatheke.

Malangizo ochepetsera kuipitsidwa kosungidwa

Sungani mbewu pamalo wouma.

• Matumba asanjidwe pamwamba pa matabwa kuti asachite chinyezi.

Onetsetsani kuti malo osungira ndiotchingidwa bwino ndi denga kuti mvula isanyowetse mbeu. Onetsetsani kuti zipinda zosungiramo zinthu zaukhondo kuti mupewe kuipitsidwa kuchokera mmbuyomu.

• Pogwiritsani ntchito zida zabwino zosungiramo, matumba okhala ndi mipata ndi oyenera kwambiri. Ngati matumba a nayiloni agwiritsidwa ntchito mabowo ena owonjezera amafunika kuti azitha kuyendetsa bwino mpweya kapena kusungiramo kwa nthawi yochepa chabe.

Onetsetsani kuti mtedza suwukulumidwa ndi tizilombo komanso makoswe kuti muchepetse kuwonongeka.

• Onetsetsani kuti malo osungirapo mbeu amapita bwino mpweya.